bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 15
Exodus 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 16 →
1
Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.
2
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
3
Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake.
4
“Chauta adaponya m'nyanja magaleta a Farao pamodzi ndi gulu lake lankhondo, adammizira atsogoleri ake amphamvu m'Nyanja Yofiira.
5
Nyanja yozamayo idaŵaphimba onse, adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala.
6
Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.
7
Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana. Ukali wanu woyaka ngati moto ukuŵatentha ngati mapesi.
8
Mutauzira mpweya wanu, madzi adaunjikana pa malo amodzi. Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma. Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake.
9
Mdani uja adati, ‘Ndidzaŵalondola nkuŵagwira. Chuma chao ndidzachigaŵagaŵa, ndipo mtima wanga udzakhutira nacho. Ndidzasolola lupanga, ndipo ndidzaŵaononga ndi dzanja langa.’
10
Koma Inu mudangouzira ndi mphepo yanu, ndipo nyanja idaŵamiza. Adangomira ngati chitsulo mpaka pansi pa madzi.
11
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
12
Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja, ndipo nthaka idaŵameza.
13
“Koma anthu amene mudaŵaombola, mudaŵatsogolera ndi chikondi chanu chosasinthika. Mudaŵatsogolera ku malo anu oyera ndi mphamvu zanu.
14
Anthu a mitundu ina amva mbiriyi, ndipo anjenjemera ndi mantha. Mantha oopsa aŵagwira Afilisti.
15
Tsopano lino mafumu a ku Edomu ataya mtima. Atsogoleri a ku Mowabu ayambapo kunjenjemera. Onse a ku Kanani agooka m'nkhongono.
16
Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa. Iwo akhala chete ngati mwala, chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu. Angokhala chete mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola, anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo.
17
Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga.
18
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.”
19
Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo.
20
Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina.
21
Ndipo Miriyamu adaŵaimbira iwowo nyimbo yakuti, “Imbirani Chauta chifukwa wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo ake omwe.”
22
Tsono Mose adatsogolera Aisraele ku Nyanja Yofiira kuja nakaloŵa m'chipululu cha Suri. Adayenda m'menemo masiku atatu, osapeza madzi.
23
Ndipo adakafika ku Mara, koma kumeneko madzi ake anali oŵaŵa, kotero kuti sadathe kuŵamwa. Nchifukwa chake malowo adaŵatcha kuti Mara.
24
Apo anthu aja adadandaulira Mose, namufunsa kuti, “Kodi ife timwa chiyani?”
25
Tsono Mose adapemphera dzolimba kwa Chauta, ndipo Chauta adamuwonetsa kamtengo. Mose adaponya kamtengoko m'madzi, ndipo madziwo adaleka kuŵaŵako. Kumeneko Chauta adapatsa anthuwo lamulo lokhazikika, ndipo adaŵayesanso komweko.
26
Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”
27
Pambuyo pake adakafika ku Elimu kumene kunali akasupe khumi ndi aŵiri, ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri. Tsono adamanga mahema ao kumeneko pafupi ndi madzi.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40