bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 11
Exodus 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 12 →
1
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tsopano ndimlanga kamodzi kokha Farao, pamodzi ndi Aejipito onse. Pambuyo pa chilango chimenechi, adzakulolani kuti muchoke. Zoonadi, akadzakulolani kuti muchoke, adzachita chokupirikitsani kuno.
2
Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.”
3
Ndipo Chauta adafeŵetsa Aejipito kuti akomere Aisraele mtima. Chinanso nkuti Mose anali wotchuka kwambiri m'dziko la Ejipito, pamaso pa nduna za Farao ndiponso pamaso pa anthu onse.
4
Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Ndiyenda pakati pa Aejipito pakati pa usiku,
5
ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso.
6
M'dziko lonse la Ejipito mudzakhala maliro okhaokha amene sadaonekepo nkale lonse, ndipo sadzaonekanso.
7
Koma pakati pa Aisraele, ndi galu yemwe sadzauwa munthu kapena choŵeta chilichonse, kuti mudziŵe kuti Chauta amasiyanitsa Aejipito ndi Aisraele.
8
Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine kudzandigwadira, zidzati, “Chokani inu pamodzi ndi anthu anu onse!” Tsono pambuyo pake, ndidzachoka.’ ” Mose adachoka kwa Farao kuja mokwiya kwambiri.
9
Chauta adauza Mose kuti, “Farao sadzakumvera iwe, kuti pakutero, Ine ndichite zozizwitsa m'dziko la Ejipito.”
10
Motero Mose ndi Aroni adachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao. Koma Chauta adamuumitsa mtima Faraoyo, ndipo Aisraelewo sadaŵalole kuti achoke m'dziko mwake.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40