bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 10
Exodus 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 11 →
1
Chauta adauza Mose kuti, “Upite kwa Farao. Ndamuumitsa mtima iyeyo ndi nduna zake, kuti ndichite zozizwitsa zonsezi pakati pao.
2
Ndipo inu, mudzaŵauze ana anu ndi zidzukulu zanu za m'mene ndidapusitsira Aejipito, pamene ndinkachita zozizwitsa pakati pao. Motero nonsenu mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
3
Mose ndi Aroni adapita kwa Farao kukamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Ahebri, akufunsa kuti, ‘Kodi udzakanabe kundigonjera mpaka liti? Uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.
4
Ukakanabe kuŵalola kuti apite, ndikugwetsera dzombe maŵa m'dziko mwako.
5
Nthaka yonse idzaphimbidwa ndi dzombelo, ndipo nthakayo sidzaoneka konse. Lidzadya zonse zomwe sizidaonongeke ndi matalala aja. Lidzadya mitengo yako yonse.
6
Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja.
7
Nduna za Farao zidafunsa Faraoyo kuti, “Kodi munthu ameneyu adzaleka liti kutivuta chotere? Aloleni anthuwo kuti apite, akapembedze Chauta, Mulungu wao. Kodi simukuwona kuti dziko la Ejipito latheratu kuwonongeka tsopano?”
8
Motero Farao adaitananso Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta, Mulungu wanu. Koma tsono apite ndani?”
9
Mose adayankha kuti, “Tidzapita tonse ndi ana athu, pamodzi ndi nkhalamba zathu zomwe. Tidzapita ndi ana aamuna, ana aakazi, nkhosa zathu ndi mbuzi zomwe. Tidzatenganso ndi ng'ombe zomwe, chifukwa choti tikachita mwambo wachipembedzo wolemekeza Chauta.”
10
Choncho Farao adaŵauza kuti, “Chauta akhale nanu ngati ine ndikulolani kuti mutenge akazi anu ndi ana anu. Nchodziŵikiratu kuti inu mukufuna kudzetsa mavuto.
11
Ai! Inu, amuna nokhanu, ndiye mupite mukapembedze Chauta, popeza kuti ndi zimene mukufuna.” Atangomveka mau ameneŵa, Mose ndi Aroni adapirikitsidwa pamaso pa Farao.
12
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Ejipito kuti dzombe libwere, ndipo lidzadye zomera zonse zimene matalala aja adasiya.”
13
Choncho Mose adakweza ndodo yake kumwamba, ndipo Chauta adautsa mphepo yakuvuma kuti iwombe pa dziko usana ndi usiku womwe. Pamene kunkacha, nkuti ponseponse pali dzombe lokhalokha.
14
Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso.
15
Lidangophimba nthaka yonse, ndipo nthakayo idada kuti bii chifukwa cha dzombelo. Lidadya kalikonse komera pa nthaka, pamodzi ndi zipatso zam'mitengo zimene matalala adasiyako. Palibe chachiŵisi chilichonse chimene chidatsalako pa mtengo kapena pa chomera chilichonse m'dziko lonse la Ejipito.
16
Ndipo Farao adaitana Mose ndi Aroni mofulumira naŵauza kuti, “Ndachimwira Chauta, Mulungu wanu, ndipo ndachimwiranso inu.
17
Koma pepani tsopano, khululukireni pa nthaŵi ino yokha, mupemphe kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti andichotsere chilango choopsachi.”
18
Mose adachoka kwa Farao kuja, nakapemphera kwa Chauta.
19
Chauta adasintha mphepoyo kuti ikhale mphepo yamkuntho yakuzambwe, ndipo idapirikitsira dzombelo ku Nyanja Yofiira. Palibe dzombe ndi limodzi lomwe limene lidatsalako ku Ejipito kuja.
20
Koma Chauta adamuumitsabe mtima Farao, ndipo sadaŵalole Aisraele kuti apite.
21
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti pagwe mdima wandiweyani pa dziko lonse la Ejipito.”
22
Mose adakweza dzanja lake kumwamba, ndipo pa masiku atatu, mudagwa mdima wandiweyani m'dziko lonse.
23
Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku.
24
Apo Farao adaitana Mose namuuza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta. Mupite nawonso akazi anu ndi ana anu omwe. Koma nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zomwe, zidzasungidwa konkuno.”
25
Mose adati, “Tsonotu muyenera kutipatsa ndinu zokaperekera nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wathu.
26
Koma iyai, zoŵeta zathu zidzapita nafe limodzi ndipo sipadzatsala choŵeta nchimodzi chomwe kuno. Tiyenera kukasankha zoŵeta zokapembedzera nazo Chauta, Mulungu wathu. Mpaka tikafike kumeneko, sitingadziŵe zoyenera kuzigwiritsa ntchito popembedza Chauta.”
27
Koma Chauta adaumitsa Farao mtima, ndipo sadalole kuti anthuwo apite.
28
Farao adauza Mose kuti, “Choka apa. Chenjera, ndipo usafikenso pamaso panga, chifukwa tsiku lomwe ndidzakuwonelo, udzaphedwa ndithu.”
29
Mose adayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, ine sindidzakuwonaninso.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40