bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 35
Exodus 35
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 36 →
1
Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti, “Chauta akukulamulani kuti,
2
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.
3
Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.”
4
Mose adauza Aisraele onse aja kuti, “Chauta akukulamulani kuti,
5
‘Muzipereka zopereka kwa Chauta. Tsono aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka, azibwera ndi zopereka izi: golide, siliva, mkuŵa,
6
thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Azibweranso ndi nsalu yokoma yabafuta, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi,
7
chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, zikopa zambuzi, matabwa a mtengo wa kasiya,
8
mafuta anyale, zonunkhira zopangira mafuta odzozera, ndiponso zopangira lubani wonunkhira bwino,
9
miyala ya mtundu wa onikisi ndi ina yokoma yoika pa chovala chaunsembe cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.’ ”
10
“Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula.
11
Apange chihema cha Chauta, hema lake pamodzi ndi chophimbira chake, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake pamodzi ndi masinde ake omwe.
12
Apangenso bokosi lachipangano ndi mphiko zake, chivundikiro chake cha bokosilo ndi nsalu zotchinga bokosilo;
13
tebulo, pamodzi ndi mphiko zake ndi zipangizo zake, ndiponso buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu;
14
choikaponyale ndi zipangizo zake, nyale zake ndi mafuta a nyalezo;
15
guwa lofukizirapo lubani ndi mphiko zake, mafuta odzozera, lubani wa fungo lonunkhira bwino, ndiponso nsalu zochingira za pa chipata cha chihema cha Chauta.
16
Apangenso guwa la zopereka zopsereza pamodzi ndi chitsolo cha sefa yamkuŵa, mphiko zake ndi zipangizo zake zomwe, beseni losambira ndi phaka lake lomwe;
17
nsalu zochinga bwalo, nsanamira pamodzi ndi masinde ake omwe, nsalu za pa chipata choloŵera ku bwalo,
18
zikhomo zake pamodzi ndi zingwe za chihema cha Chauta ndi za bwalo lake;
19
nsalu zokoma kwambiri zovala anthu otumikira m'malo opatulika, ndiponso zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, akamatumikira ngati ansembe.”
20
Tsono Aisraele onse aja adachoka ndi kumsiya Mose.
21
Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika.
22
Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
23
Munthu aliyense amene anali ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, bafuta wa thonje losalala kwambiri, nsalu za ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi zikopa zambuzi, adabwera nazo kwa Chauta. Aliyense adabwera ndi zimene anali nazo.
24
Anthu onse amene anali ndi siliva kapena mkuŵa, zonsezo adabwera nazo kwa Chauta. Onse amene anali ndi matabwa a mtengo wa kasiya wogwiritsira ntchito pomangapo, adabwera nawo ndithu.
25
Akazi onse aluso adaomba nsalu za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Adabweranso ndi bafuta wa thonje losalala kwambiri.
26
Akazi onse alusowo adaombanso nsalu za ubweya wambuzi.
27
Ndipo atsogoleri adabwera ndi miyala ya onikisi ndi miyala ina yoika pa chovala cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.
28
Adaperekanso zonunkhira, mafuta anyale, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma.
29
Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta.
30
Pambuyo pake Mose adauza Aisraele kuti, “Chauta wasankhula Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda.
31
Chauta wadzaza Bezaleleyo ndi mzimu wa Mulungu, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndiponso ndi wodziŵa ntchito zonse zaluso.
32
Amadziŵanso kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa.
33
Amadziŵa kusema miyala yakongoletsera, kujoba matabwa, ndi kuchita ntchito zonse zaluso.
34
Tsono Chauta wapatsa nzeru kwa iyeyo ndi kwa Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, kuti aziphunzitsa ena luso laolo.
35
Iwoŵa adapatsidwa luso lalikulu, kuti achite ntchito za mitundu yonse zimene amachita anthu ozokota, amisiri a ntchito zaluso, anthu oomba nsalu za bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akudziŵadi kugwira ntchito zonse, ndipo angathenso kuganizira ntchito zonse zaluso.
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→