bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 3
Exodus 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 4 →
1
Mose ankaŵeta ziŵeto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina adatenga ziŵetozo, nayenda nazo cha kuzambwe kwa chipululu, mpaka kukafika ku phiri la Mulungu dzina lake Horebu.
2
Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malaŵi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto laŵilaŵi, koma osapsa.
3
Tsono mumtima mwake adati, “Ndipita pafupi, kuti ndikaonetsetse zozizwitsa ndikupenyazi. Chifukwa chiyani chitsambacho sichilikupsa?”
4
Chauta ataona kuti Mose akuyandikira, adamuitana m'chitsambamo kuti, “Mose, Mose!” Mose adayankha kuti “Ŵaŵa.”
5
Mulungu adati, “Usayandikire pafupi. Vula nsapato zakozo, chifukwa malo waimapowo ngoyera.”
6
Adapitirira kunena kuti, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.” Pompo Mose adadziphimba kumaso chifukwa adaopa kupenya Mulungu.
7
Kenaka Chauta adati, “Ndaona m'mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuŵapsinja. Ndikudziŵa bwino kuzunzika kwao.
8
Ndabwera kuti ndiŵapulumutse kwa Aejipito ndi kuŵatulutsa m'dziko limenelo, kuti ndikaŵaloŵetse m'dziko lalikulu lachonde. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Amene akukhala m'dziko limenelo ndi Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
9
Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraele, ndipo ndaŵaonadi mazunzowo amene Aejipito akuŵapsinja nawo.
10
Tsono iwe ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga Aisraele ku Ejipito.”
11
Apo Mose adafunsa kuti, “Kodi ndine yani ine, kuti ndingapite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraele ku Ejipito?”
12
Mulungu adamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe. Chitsimikizo chakuti ndakutuma ndine nachi: Utaŵatulutsa anthu anga ku Ejipito, mudzandipembedza pa phiri lomwe lino.”
13
Mose adayankha kuti, “Tsono ine ndikapita kwa Aisraelewo kukaŵauza kuti Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu, iwowo akakandifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndiye ineyo ndikaŵauze chiyani?”
14
Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
15
Ndipo Mulungu adamuuzanso Mose kuti, “Aisraele ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, ndiye amene wandituma kwa inu. Tsono limeneli ndilo dzina langa mpaka muyaya. Limeneli ndilo dzina limene idzanditchula mibadwo yonse yam'tsogolo.
16
Pita ukaŵasonkhanitse atsogoleri onse a Aisraele, ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adandiwonekera; adandilamula kuti ndikuuzeni kuti wabwera kwa inu, ndipo zonse zimene akukuchitani Aejipito, waziwona.
17
Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.”
18
Mulungu adapitirira kunena kuti, “Zimene ukaŵauzezo, adzamva. Ndiye mukapite kwa mfumu ya ku Ejipito, iwe ndi atsogoleri a Aisraelewo, ndipo mfumuyo mukaiwuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, adakumana nafe. Tsono tikukupemphani, mutilole kuti tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu.’
19
Kudziŵa ndikudziŵa kuti mfumu ya ku Ejipitoyo sidzakulolani kuti mupite, mpaka nditaikakamiza kutero.
20
Tsono Ine ndidzagwiritsa ntchito mphamvu zanga ndipo ndidzalanga Ejipito ndi zozizwitsa zomwe ndidzachite kumeneko. Zikadzachitika zimenezo, adzakulolani.
21
Aejipito ndidzaŵafeŵetsa mtima pa anthu anga, kotero kuti pamene muzidzachoka, simudzapita chimanjamanja.
22
Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→