bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 30
Exodus 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 31 →
1
“Tsono upange guwa lofukizirapo lubani. Upange guwalo ndi matabwa a mtengo wa kasiya.
2
Likhale lalibanda, kutalika kwake masentimita 46, muufupi mwake likhalenso masentimita 46, ndipo msinkhu wake ukhale wa masentimita 91. Nyanga zake zipangidwire kumodzi ndi guwalo.
3
Ulikute ndi golide pamwamba pake, pa mbali zake zonse zinai ndi pa nyanga zakezo. Ndipo kuzungulira guwa lonselo ulembe mkombero wagolide.
4
Upange mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo uzilumikize ku guwa m'munsi mwa mkombero pa mbali ziŵiri, kuti mphiko zipisidwe m'mphetezo.
5
Mphiko zimenezi ikhale ya mtengo wa kasiya, ndipo uikute ndi golide.
6
Guwalo ulikhazike patsogolo pa nsalu yochinga bokosi lachipangano, patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa bokosi lachipangano. Pa malo ameneŵa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
7
M'maŵa mulimonse Aroni azifukiza lubani wa fungo lokoma, ndipo nthaŵi yomweyo azikonza nyale zija.
8
Tsono pamene ayatsa nyalezo madzulo, azifukizanso lubani. Choncho pakhale kufukiza kosalekeza pamaso pa Chauta m'mibadwo yanu yonse.
9
Paguwapo usafukizepo lubani wosaloledwa, kapena zopereka za nyama yopsereza kapena za zakudya. Usadzaperekenso pamenepo chopereka cha chakumwa.
10
Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.”
11
Chauta adapitiriza kuuza Mose kuti,
12
“Ukamachita kalembera wa ana aamuna a Aisraele, munthu aliyense adzapereke kwa Chauta choombolera moyo wake, kuti mliri uliwonse usadzamugwere pamene kalemberayo akuchitika.
13
Aliyense woyenera kulembedwa m'kalemberamo adzapereke theka la sekeli, ndiye kuti ndalama zolemera ngati magaramu asanu ndi limodzi, kutsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu (paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi aŵiri). Ndalama zimenezi zidzakhala zopereka kwa Chauta.
14
Aliyense wolembedwa m'kalemberamo, wa zaka makumi aŵiri kapena kupitirira, adzapereke zimenezi kwa Chauta.
15
Wolemera asadzapereke kopitirira, ndipo wosauka asadzapereke mochepera pa theka la sekeli, pamene muzikapereka kwa Chauta zopereka zimenezi, kuti muwombole moyo wanu.
16
Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.”
17
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
18
“Upange beseni lamkuŵa losambira, ndipo phaka lake likhale lamkuŵa. Ulikhazike pakati pa chihema chamsonkhano ndi guwa, ndipo uthiremo madzi.
19
Aroni ndi ana ake azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi ao ndi madzi amenewo.
20
Akamaloŵa m'chihema chamsonkhano, kapena kuyandikira guwalo pa ntchito yao yautumiki, ndi kumapereka kwa Chauta chopereka chopsereza, sadzafa malinga akasamba ndi madzi amenewo.
21
Azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi, kuti angafe. Limeneli ndi lamulo ndithu limene iwowo ndi adzukulu ao akutsogolo ayenera kumadzalitsata mpaka muyaya.”
22
Chauta adauzanso Mose kuti,
23
“Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino,
24
makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi.
25
Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.
26
Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano,
27
tebulo ndi zipangizo zake zonse, choikaponyale pamodzi ndi zida zake, guwa lofukizirapo lubani,
28
guwa lopserezapo zopereka, pamodzi ndi zipangizo zake, ndiponso beseni losambiramo lija ndi phaka lake lomwe.
29
Zonsezi udzazipatula mwa njira imeneyi, ndipo zidzakhala zoyera kopambana. Ndipo chilichonse chokhudza zimenezi chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
30
Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira.
31
Tsono Aisraele onse udzaŵauze kuti, ‘Ameneŵa ndiwo adzakhale mafuta anga oyera odzozera pa mibadwo yanu yonse.
32
Musadzadzozere anthu wamba, ndipo musadzapangenso mafuta ena ofanafana nawo. Ameneŵa ngoyera ndipo kwa inu adzakhalabe oyera ndithu.
33
Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ”
34
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge miyeso yofanafana ya zonunkhira bwino izi: sitakate, onika, galibanumu, ndi lubani weniweni.
35
Uphatikize pamodzi zonsezi, ndipo upange lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athiremo mchere, ndipo akhale woyera ndi wopatulika.
36
Upere gawo lina mosalala kwambiri, ndipo utatapako pang'ono, uike patsogolo pa bokosi lachipangano m'chihema chamsonkhano chokumanirako ndi anthu anga. Lubani ameneyu kwa inu akhale woyera kopambana.
37
Ndipo lubani amene upangeyo potsata mapangidwe ake, asadzakhalire inuyo ai, koma adzakhale woyera wokhalira Chauta yekha.
38
Ngati munthu wina apanga lubani wofanafana ndi ameneyu kuti amve fungo lake lokoma, azichotsedwa pakati pa anthu anzake.”
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→