bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 13
Exodus 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 14 →
1
Chauta adauzanso Mose kuti,
2
“Ana onse achisamba uŵapereke kwa Ine. Pakati pa Aisraele mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kaya ndi wa munthu kaya ndi wa nyama, ndi wanga ameneyo.”
3
Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa.
4
Mukuchoka ku Ejipito pa tsiku lalero, mwezi uno wa Abibu.
5
Chauta adalonjeza makolo anu kuti adzakupatsani dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Akadzakuloŵetsani m'dziko limenelo, muzidzachita mwambo umenewu mwezi uno.
6
Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidzadya buledi wosafufumitsa, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo pazidzakhala chikondwerero cha Chauta.
7
Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pasamadzakhala buledi wofufumitsa, kapena chofufumitsira chilichonse m'dziko lanu lonselo.
8
Pa tsiku limenelo muzidzauza ana anu kuti, ‘Tikuchita zonsezi chifukwa cha zimene Chauta adatichitira pamene tinkachoka ku Ejipito.’
9
Lamulo limeneli lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa padzanja panu, kapena chikumbutso chomangidwa pamphumi panu. Motero malamulo a Chauta sadzachoka konse pakamwa panu, chifukwa Iye adakutulutsani ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu.
10
Musunge malangizo ameneŵa pa nthaŵi yake chaka ndi chaka.
11
“Chauta adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani limene adakulonjezani pamodzi ndi makolo anu. Akadzakupatsani dziko,
12
muzidzapereka kwa Chauta chilichonse choyamba kubadwa. Zoŵeta zanu zamphongo zoyamba kubadwa nza Chauta zimenezo.
13
Koma mwanawabulu woyamba kubadwa, muzimuwombolanso pakupereka mwanawankhosa m'malo mwake. Ngati simufuna kumuwombola, muzimthyola khosi. Muziwombola mwana wamwamuna wachisamba aliyense.
14
M'tsogolo mwana wanu wamwamuna adzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Pamenepo inu mudzayankhe kuti, ‘Chauta adatitulutsa ku Ejipito, ku dziko laukapolo, ndi dzanja lake lamphamvu.
15
Farao atauma mtima ndithu, natikaniza kuchoka, Chauta adapha mwana wachisamba aliyense wamwamuna m'dziko lonse la Ejipito. Adapha ana a anthu ndi a zoŵeta omwe. Nchifukwa chake nyama yamphongo iliyonse yoyamba kubadwa imaperekedwa nsembe kwa Chauta. Koma ana athu achisamba aamuna, timachita choombola.
16
Chimenechi chidzakhala chikumbutso, monga ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu kapena pamphumi panu, chifukwa Chauta adatitulutsa ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu.’ ”
17
Farao ataŵalola Aisraele kuti apite, Mulungu sadaŵadzeretse njira yopita kwa Afilisti, ngakhale kuti imeneyi inali njira yachidule. Mulungu adati, “Sindifuna kuti anthu ameneŵa adzasinthe maganizo ao nadzabwereranso ku Ejipito, akadzangokumana ndi nkhondo yolimbana nawo.”
18
M'malo mwake Mulungu adaŵadzeretsa njira yozungulira, yachipululu, yopita ku Nyanja Yofiira. Monsemo nkuti Aisraele ali okonzekeratu za nkhondo.
19
Mose adanyamula mafupa aja a Yosefe, chifukwa Yosefeyo anali atalumbiritsa Aisraele aja kuti ndithu mafupawo adzanyamule. Paja Yosefe adaanena kuti, “Ndithu, Mulungu adzakuthandizani, koma mudzayenera kunyamula mafupa angaŵa kuchoka nawo kuno.”
20
Aisraele adachoka ku Sukoti, nakagona ku Etamu m'mbali mwa chipululu.
21
Nthaŵi yamasana Chauta ankaŵatsogolera ndi chipilala chamtambo namaŵalangiza njira. Ndipo nthaŵi yausiku, ankaŵatsogolera ndi chipilala chamoto, kuŵaunikira njira kuti aziyenda masana ndi usiku womwe.
22
Nthaŵi zonse chipilala chamtambo chinkatsogolera anthu masana, ndipo chipilala chamoto chinkaŵatsogolera usiku.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40