bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 27
Exodus 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 28 →
1
“Upange guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda: muutali mwake likhale masentimita 229, muufupi mwake chimodzimodzi: masentimita 229, msinkhu wake masentimita 137.
2
Upange nyanga pa ngodya zake zinaizo, zilumikizane ndi guwalo, ndipo ulikute ndi mkuŵa.
3
Upangenso mbale zake zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, mafoloko aakulu ndiponso ziŵiya zosonkhapo moto. Zipangizo zonse za ku guwalo zikhale zamkuŵa.
4
Upangenso chitsulo chamkuŵa choboolaboola ngati sefa. Pa ngodya zake za chitsulocho upange mphete zamkuŵa zonyamulira.
5
Uike sefayo m'munsi mwake mwa chibumi cha guwalo, ndipo ilekeze pakati pa guwalo.
6
Upange mphiko ya mtengo wa kasiya yonyamulira guwalo, ndipo uikute ndi mkuŵa.
7
Ponyamula guwalo, mphikozo azizipisa m'mphete za pa mbali ziŵiri za guwalo.
8
Ndipo guwalo udzalipange mogoba m'kati mwake. Ulipange monga momwe ndikukulangizira paphiri pano.
9
“Pambuyo pake upange bwalo la chihema, lochingidwa. Chakumwera kwake kukhale nsalu zochinga za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, kutalika kwa mbali imodzi kukhale mamita 46.
10
Nsanamira zake 20 ndi masinde ake 20 zikhale zamkuŵa, koma ngoŵe za nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zikhale zasiliva.
11
Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
12
Muufupi mwake mwa bwalolo cha mbali yakuzambwe, pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira khumi ndi masinde khumi.
13
Chakuvuma, komwe kuli chipata chake, bwalolo likhalenso mamita 23 muufupi mwake.
14
Pa mbali ina ya chipata pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.
15
Chimodzimodzi pa mbali ina pakhalenso nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.
16
Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anai. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai.
17
Nsanamira zonse kuzungulira bwalolo zilumikizidwe ndi mitanda yasiliva, ndipo ngoŵe zake zikhalenso zasiliva, koma masinde ake akhale amkuŵa.
18
Kutalika kwake kwa bwalolo kukhale mamita 46, muufupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu zochingazo zikhale za thonje losankhidwa bwino kwambiri ndi lopikidwa, ndipo masinde ake akhale amkuŵa.
19
Zipangizo zonse zogwiritsira ntchito zosiyanasiyana m'chihemamo, pamodzi ndi zikhomo za chihemacho ndi za bwalolo, zonsezo zikhale zamkuŵa.
20
“Uŵalamule Aisraele kuti akupatse mafuta aolivi opsinyidwa bwino, oyatsira nyale, kuti ziziyaka kosalekeza.
21
Aroni ndi ana ake aamuna aziyatsa nyale m'chihema chamsonkhanomo amakumana ndi anthu ake, kunja kwa chochinga, patsogolo pa miyala yaumboni ija. Tsono nyalezo ziziyaka kumeneko kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Lamulo limeneli adzalisunge Aisraele ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40