bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 39
Exodus 39
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 40 →
1
Tsono adapanga zovala zokongola kwambiri za ansembe, zovala potumikira m'malo oyera. Adapanga zovalazo ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira. Adapanga zovala za Aroni monga momwe Chauta adalamulira Mose.
2
Adapanga chovala chopatulika cha efodi ndi nsalu yagolide ndiponso ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
3
Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri.
4
Tsono adapanga tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, tolumikizika ku chovalacho pa mbali zake ziŵiri.
5
Panalinso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso anali wa nsalu yagolide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
6
Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele.
7
Yonseyo adaiika pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, kuti iziŵakumbutsa ana a Israele, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
8
Pambuyo pake adapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri, monga chovala cha efodi chija. Adachipanga ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira, ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
9
Kutalika kwake kwa chovala chapachifuwacho kunali masentimita 23, muufupi mwakenso masentimita 23, ndipo chinali chopinda paŵiri.
10
Tsono adaikapo mizere inai ya miyala yokongola. Pa mzere woyamba adaika miyala ya rubi, topazi ndi garaneti.
11
Pa mzere wachiŵiri adaika miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi.
12
Pa mzere wachitatu adaika miyala ya opela, agate ndi ametisiti,
13
ndipo pa mzere wachinai adaika miyala ya berili, onikisi ndi yasipara. Miyalayo adaiika m'zoikamo zagolide.
14
Panali miyala khumi ndi iŵiri imene adalembapo maina a mafuko a Israele. Inali miyala khumi ndi iŵiri yozokotedwa ngati zidindo, ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina la fuko limodzi.
15
Adapanga timaunyolo ta chovala chapachifuwa ta golide wabwino kwambiri, topota mwaluso ngati maukufu.
16
Adapanganso zoikamo zake ziŵiri zagolide zonga maluŵa, ndiponso mphete ziŵiri, ndipo adalumikiza mphete ziŵirizo ku nsonga zake zapamwamba za chovala chapachifuwacho.
17
Tsono zingwe ziŵiri zagolide adazilumikiza ku mphete ziŵiri zija,
18
ndi kulumikiza nsonga ziŵiri zina za zingwezo m'zoikamo zake ziŵiri zija. Motero adazilumikiza patsogolo pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija.
19
Adapanga mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku nsonga ziŵiri za chovala chapachifuwa cham'mphepete, m'kati mwake, pafupi ndi chovala cha efodi chija.
20
Adapanganso mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku mbali yam'munsi, kutsogolo kwa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, pafupi ndi msoko, ndiponso pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja wa efodiyo.
21
Ndipo adalumikiza mphete za chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi. Adalumikiza ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja, ndipo chisalekane ndi efodi ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
22
Adapanga mkanjo wake wa efodi, woombedwa ndi nsalu yobiriŵira.
23
Mkanjowo unali ndi popisa mutu, ndipo maonekedwe ake anali ngati popisa mutu pa malaya. M'mbali mwake kuzungulira, munali mosokerera bwino, kuti ungang'ambike.
24
Pa mpendero wake wapansi, adalumikizapo zithunzi za makangaza zopangidwa ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
25
Adapanganso timabelu ta golide wabwino kwambiri, mopakiza pakati pa makangazawo, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo.
26
Tsono panali khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wa mkanjo, umene ansembe ankavala pogwira ntchito zaunsembe, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
27
Tsono Aroni ndi ana ake, amisiri aja adaŵapangira miinjiro,
28
nduŵira, makofiya ndi akabudula, zonsezo zopangidwa ndi nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
29
Adapanganso lamba wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino ndi wa thonje lobiriŵira, lofiira ndi lofiirira, ndipo adamkongoletsa ndi zopetapeta, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
30
Ndipo adapanga duŵa la golide wabwino kwambiri. Limenelo linali chizindikiro chopatulika, ndipo mofanizira ndi mazokotedwe a chidindo, adazokotapo mau akuti, “Chopereka kwa Chauta.”
31
Kenaka adatenga kamkuzi kobiriŵira namangirira duŵa limenelo ku nsalu ya nduŵira ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
32
Tsono ntchito yonse yomanga chihema chamsonkhano idatha. Aisraele aja adachitadi zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
33
Pambuyo pake zonsezo adabwera nazo kwa Mose: chihema chija chodzakhala Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake ndi masinde ake omwe.
34
Adabweranso ndi chophimbira cha chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, chophimbira cha chikopa chambuzi, nsalu zochingira,
35
bokosi loikamo miyala yaumboni pamodzi ndi nsanamira zake, ndiponso chivundikiro cha bokosilo.
36
Adabweranso ndi tebulo, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo adaika buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu;
37
choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale;
38
guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani wa fungo lokoma, nsalu yotsekera pa chipata choloŵera m'chihema,
39
guwa lamkuŵa, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, mphiko zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso beseni losambira ndi phaka lake.
40
Adabweranso ndi nsalu zochingira bwalo pamodzi ndi nsanamira zake ndi masinde ake, nsalu yochingira pa chipata choloŵera m'bwalolo, pamodzi ndi zingwe zake ndi zikhomo zake, ndiponso zipangizo zonse zotumikira nazo m'chihema cha Chauta chija.
41
Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe.
42
Motero Aisraele adachitadi ntchito zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
43
Tsono Mose adaona zonse zimene zidapangidwazo, ndipo adatsimikiza kuti adazipangadi monga momwe Chauta adalamulira. Pamenepo Mose adaŵadalitsa anthu onsewo.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40