bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 8
Exodus 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 9 →
1
Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, Chauta akuti, ‘Uŵalole anthu anga apite akandipembedze.
2
Ukakana kuŵalola, dziko lako lonse ndidzalilanga polidzaza ndi achule.
3
Mtsinje uja udzakhala wodzaza ndi achule. Adzachokera mumtsinjemo namakaloŵa m'chipinda mwako mogona, pabedi pako, m'nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, m'malo onse ophikira ndi mophikira buledi momwe.
4
Azidzakulumphira iwe, pamodzi ndi anthu ako, ndi nduna zako zonse.’ ”
5
Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Uloze ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Aejipito.’ ”
6
Choncho Aroni adaloza ndodo yake pa madzi, ndipo achule adatuluka, nadzaza dziko lonselo.
7
Koma amatsenga aja nawonso adapanga ao achule ndipo adayamba kukwera pa mtunda.
8
Pomwepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pempherani kwa Chauta kuti achuleŵa andichoke ine ndi anthu angaŵa, ndipo ndidzaŵalola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Chauta.”
9
Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chabwino, mungondiwuza nthaŵi yoti ndikupempherereni inu, nduna zanu ndi anthu anu omwe, kuti achuleŵa akuchokeni, achokenso m'nyumba mwanu, ndipo kuti akakhale mumtsinje mokha.”
10
Farao adati, “Maŵa.” Apo Mose adati, “Zidzachitika monga momwe mwaneneramu, ndipo mudzadziŵa kuti palibe Mulungu wina wofanafana ndi Chauta, Mulungu wathu.
11
Achulewo adzakuchokani, adzachokanso m'nyumba zanu, m'nyumba za nduna zanu, ndipo azidzangokhala mumtsinje mokha.”
12
Pamenepo Mose ndi Aroni adachoka kwa Farao kuja, ndipo adakapempha Chauta kuti achotse achule amene adaatumiza kwa Farao aja.
13
Tsono Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Motero achule onse aja amene adaali m'nyumba, pa bwalo ndi m'minda momwe, adafa.
14
Aejipito aja adaŵaunjika achulewo milumilu, ndipo dziko lonse lidadzaza ndi chivunde chokhachokha.
15
Farao ataona kuti zinthu zayamba kukhala bwino, adaumitsa mtima wake, ndipo sadafunenso kumvera Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.
16
Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.”
17
Iwowo adachitadi momwemo. Aroni adasamula ndodo yake ija namenya nthaka. Tsono fumbi lonse lidasanduka nthata, ndipo zidabalalikira pa anthu ndi pa nyama zomwe. Motero fumbi lonse la ku Ejipito lidangokhala nthata zokhazokha.
18
Amatsenga aja adayesanso momwemo mwa matsenga ao kuti apange zao nthata, koma adalephera. Ndipo nthatazo zidabalalikira pa anthu ndi nyama zomwe.
19
Tsono amatsenga aja adauza Farao kuti, “Zimenezi wachita ndi Mulungu ndithu.” Koma Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadamvere zimene Mose ndi Aroni ankanena monga momwe Chauta adaanenera muja.
20
Apo Chauta adauza Mose kuti “Maŵa m'maŵa ndithu, upite ukakumane ndi Farao pamene akupita ku mtsinje, ukamuuze kuti, ‘Chauta akunena kuti uŵalole anthu anga apite, akandipembedze Ine.
21
Ukapanda kulola anthu anga kuti apite, ndidzatumiza mizaza pa iwe, nduna zako, anthu ako ndi m'nyumba mwako. M'nyumba zonse za Aejipito, ngakhalenso pa nthaka yonse imene akukhalapo, padzakhala mizaza yokhayokha.
22
Pa tsiku limenelo ndidzapatula dziko la Goseni lokhalamo anthu anga, mwakuti lokhalo lidzakhala lopanda mizaza, kuti iweyo udziŵe kuti Ine ndine Chauta ndipo kuti ndikulamulira pa dziko lapansi.
23
Ndidzasiyanitsa ndithu pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chozizwitsa chimenechi chichitika maŵali.’ ”
24
Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo.
25
Tsono Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapereke nsembe kwa Mulungu wanu m'dziko mommuno.”
26
Koma Mose adayankha kuti, “Sikungakhale bwino konse kuchita zimenezo, chifukwa Aejipito zidzaŵaipira nsembe zimene timapereka kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikadzapereka nsembe zimene Aejipito zimaŵanyansa m'maso mwao, kodi iwo sadzatiponya miyala mpaka kutipha?
27
Tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu, monga adatilamulira.”
28
Farao adati, “Ndidzakulolani kuti mupite mukapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku chipululu, koma musapite kutali kwambiri. Tsono mundipempherere.”
29
Apo Mose adati, “Malinga ndikachoka pano, ndikukapempha kwa Chauta, ndipo maŵa mizaza ikuchokani inu, nduna zanu ndiponso anthu anu. Koma musatinyengenso ndi kuŵaletsa anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Chauta.”
30
Mose atachoka kwa Faraoko, adakapemphera kwa Chauta.
31
Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe.
32
Koma ngakhale pa nthaŵi imeneyinso, Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadalole kuti Aisraele apite.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→