bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 23
Exodus 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 24 →
1
“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.
2
Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri.
3
Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera.
4
“Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse.
5
Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
6
“Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu.
7
Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
8
Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa.
9
“Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja.
10
“Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo.
11
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
12
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
13
Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.
14
“Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine.
15
Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.
16
Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
17
Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa.
18
“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.
19
“Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make.
20
“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.
21
Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa.
22
Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.
23
“Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo.
24
Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.
25
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
26
Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.
27
Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka.
28
Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu.
29
Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha.
30
Koma ndidzaŵapirikitsa pang'onopang'ono, mpaka mutabala ana ambiri amene angathe kutenga dzikolo,
31
kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku Nyanja Yaikulu ya Afilisti, ndi kuyambiranso ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Ndidzakupatsani mphamvu zopambanira anthu a m'dzikolo, ndipo mudzaŵapirikitsa.
32
Musadzachite nawo chipangano iwowo kapenanso milungu yao.
33
Asadzakhale m'dziko mwanu, kuwopa kuti angadzakuchimwitseni. Mukamapembedza milungu yao, ndithu mudzakodwa mu msampha.”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→