bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 1
Proverbs 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
1
Aŵa ndi malangizo a Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele.
2
Ngothandiza kuti anthu adziŵe nzeru ndi mwambo, kuti amvetse mau a matanthauzo ozama,
3
kuti alandire mwambo wochita zinthu mwanzeru, akhale angwiro, achilungamo ndi osakondera.
4
Ngophunzitsa anthu wamba nzeru za kuchenjera, ndi achinyamata kudziŵa zinthu ndi kulingalira bwino.
5
Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,
6
kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mau a anthu anzeru ndi mikuluŵiko yao.
7
Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.
8
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.
9
Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.
10
Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa, usamaŵamvera.
11
Adzati, “Tiye kuno, tikabisale kuti tiphe anthu, tiye tikalalire anthu osalakwa.
12
Tiyeni tiŵameze amoyo ngati manda, tiŵameze athunthu ngati anthu otsikira ku manda.
13
Motero tidzapata zinthu zambiri zamtengowapatali, nyumba zathu tidzazidzaza ndi zofunkha.
14
Tiye uloŵe m'gulu lathu, chuma chathu tidzagaŵana tonse.”
15
Mwana wanga, usamayenda nawo anthu amenewo, usatsagane nawo pa njira yaoyo.
16
Paja iwowo amangofuna zoipa zokhazokha, amathamangira kupha basi.
17
Nkopanda phindu kutchera kumwezi, nanga mbalame siziwona!
18
Koma anthu ameneŵa amangodzitchera okha msampha, m'menemo muli imfa yao yomwe.
19
Ameneŵa ndiwo mathero a anthu opata chuma mwankhondo. Chumacho chimapha eniake ochikundika.
20
Nzeru ikufuula mu mseu, ikulankhula mokweza mau m'misika.
21
Ikufuula pa mphambano za miseu, ikulankhula pa zipata za mzinda, kuti,
22
“Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti?
23
Musamale kudzudzula kwangaku, ine ndikuuzani maganizo anga, ndi kukudziŵitsani mau anga.
24
Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera, ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako.
25
Uphungu wanga simudaulabadire, kudzudzula kwanga simudakusamale.
26
Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto, ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha,
27
pamene mantha adzakukunthani ngati namondwe, pamene tsoka lidzakufikirani ngati kamvulumvulu, pamene mavuto ndi masautso adzakugwerani.
28
Tsono mudzandiitana, koma ine sindidzaitaŵa, mudzandifunafuna mwakhama, koma simudzandipeza.
29
Popeza kuti mudadana ndi nzeru, ndipo simudasankhe kuwopa Chauta,
30
popeza kuti simudasamale malangizo anga, ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse,
31
basitu tsono mudzadya zipatso zoyenera ntchito zanuzo, mudzakhuta zoipa zimene munkafuna kuŵachita ena.
32
Anthu opusa amaphedwa chifukwa cha kusokera kwao. Zitsiru zimadziwononga zokha nkudzitama kwao.
33
Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31