bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 18
Proverbs 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 19 →
1
Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona.
2
Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu. Koma chimangolankhula za maganizo ake okha.
3
Kuipa mtima kukaoneka, pamabweranso manyozo, kunyozeka kumaitana manyazi.
4
Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga.
5
Si kwabwino pa mlandu kukondera munthu woipa, kapena kupondereza munthu wosalakwa.
6
Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo.
7
Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.
8
Mau a kazitape ali ngati chakudya chokoma, anthu amaŵameza onse mokondwa.
9
Wogwira ntchito yake mwaulesi, ali pachibale ndi munthu woononga zinthu.
10
Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.
11
Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali limene amayesa ndi lomutchinjiriza.
12
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
13
Ukayankha usanamve nkhani yonse, umaoneka wopusa ndipo umachita manyazi.
14
Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso?
15
Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.
16
Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi, imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu.
17
Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wokhoza ndiye, mpaka mnzake atabwera nadzamufunsitsa bwino.
18
Maere amathetsa mikangano. Amalekanitsa okangana amphamvu.
19
Mnzako ukamthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumakutsekera thandizo lililonse.
20
Munthu amapeza bwino kapena ai, malinga ndi zolankhula zake, amalandira zotsatira za mau a pakamwa pake.
21
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
22
Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino, Chauta wamukomera mtima.
23
Anthu osauka amapemba, koma anthu olemera amayankha mwaukali.
24
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31