bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 23
Proverbs 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 24 →
1
Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uyang'ane bwino zimene zili pamaso pako.
2
Ngati ndiwe munthu wadyera, udziletse kuti usachite khwinthi.
3
Usasirire zakudya zake zokoma, poti zimenezi ndi zakudya zonyenga.
4
Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa.
5
Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.
6
Usadye chakudya kwa munthu waunkhambo, usamalakalaka zakudya zake zokoma.
7
Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu. Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!” Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna.
8
Udzasanza nthongo wadyazo, ndipo mau ako oshashalika adzapita pachabe.
9
Usamalankhula pali munthu wopusa, pakuti adzanyoza mau ako anzeru.
10
Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye.
11
Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo.
12
Mtima wako ukhale pa malangizo, ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru.
13
Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa.
14
Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa.
15
Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala.
16
Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama.
17
Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa, koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku.
18
Ndithu, zakutsogolo zilipo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
19
Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uuyendetse m'njira yabwino.
20
Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera.
21
Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.
22
Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba.
23
Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.
24
Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye.
25
Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe.
26
Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine, maso ako apenyetsetse njira zanga.
27
Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza.
28
Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika.
29
Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula? Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake? Ndani ali wofiira maso?
30
Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina.
31
Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero.
32
Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri.
33
Maso ako adzaona zinthu zachilendo, maganizo ndi mau ako adzakhala okhotakhota.
34
Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalaŵa.
35
Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke. Adandimenya, koma ine osamvako. Kodi ine ndidzatsitsimuka liti? Ndiye ndithamangira chakumwa china.”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31