bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 26
Proverbs 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
1
Ulemu woulandira chitsiru uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe, kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola.
2
Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha.
3
Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ncha m'kamwa mwa bulu, chonchonso ndodo ndi yoyenerera zitsiru.
4
Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho.
5
Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru.
6
Amene amatuma chitsiru kukanena uthenga, amachita ngati kudzidula mapazi ndipo amadziitanira mavuto.
7
Monga miyendo ya munthu wopunduka imakhala yopanda ntchito, ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
8
Amene amachitira chitsiru ulemu ali ngati munthu wokulunga mwala m'khwenengwe.
9
Monga imachitira minga yobaya dzanja la chidakwa ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
10
Amene amalemba ntchito chitsiru chongodziyendera kapena chidakwa, ali ngati munthu woponya mivi amene amangolasa anthu chilaselase.
11
Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake chili ngati galu wodya masanzi ake omwe.
12
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
13
Waulesi amati, “Pali mkango pa njira! Mumseumo muli mkango!”
14
Monga chitseko chimatembenukira uku ndi uku pa zomangira zake, ndimonso waulesi amangokunkhulira pabedi pake.
15
Waulesi amati akapisa dzanja lake m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake.
16
Waulesi amadziyesa wanzeru kupambana anthu asanu ndi aŵiri amene angathe kuyankha mochenjera.
17
Amene angoloŵerera ndeu ya eniake, ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera.
18
Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa,
19
ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!”
20
Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.
21
Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano.
22
Mau a kazitape ali ngati zakudya zokoma, zimene zimatsikira m'mimba msanga.
23
Monga m'mene chiziro chimakutira chiŵiya chadothi, ndimonso mau oshashalika amabisira mtima woipa.
24
Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga.
25
Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa.
26
Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu.
27
Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha, amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo.
28
Munthu wonama amadana ndi amene iye adaŵapweteka, pakamwa poshashalika mpoononga.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31