bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 27
Proverbs 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
1
Usamanyadira zamaŵa, pakuti sudziŵa zimene zidzachitika pa tsikulo.
2
Akutame ndi wina, osati pakamwa pako pomwe, wosadziŵana naye akakutamanda, apo ndipo.
3
Mwala ndi wolemera, ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
4
Mkwiyo umadzetsa nkhanza, kupsa mtima kumachititsa zoopsa, koma nsanje imabweretsa zoipa zopambana.
5
Kudzudzula munthu poyera nkwabwino kupambana kubisa chikondi chimene uli nacho.
6
Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.
7
Wokhuta amaipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ndi zoŵaŵa zomwe zimatsekemera.
8
Munthu amene wasokera kutali ndi kwao, ali ngati mbalame yosokera kutali ndi chisa chake.
9
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
10
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
11
Mwana wanga, ukhale ndi nzeru, ukondwetse mtima wanga, kuti choncho ndithe kumuyankha amene amandinyoza.
12
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
13
Munthu amene waperekera mlendo chikole, umlande chovala chake, chimenecho chikhale chigwiriro chako, chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika.
14
Wopatsa mnzake moni mofuula m'mamaŵa kwambiri, adzamuyesa kuti akutemberera.
15
Mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi.
16
Kuyesa kumletsa mkazi woteroyo kuli ngati kuyesa kuletsa mphepo, kapena kuyesa kufumbata mafuta m'manja.
17
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
18
Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake, chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu.
19
Monga momwe nkhope imaonekera m'madzi, momwemonso mtima wa munthu umadziŵika ndi zochita zake.
20
Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta.
21
Siliva amasungunulira mu uvuni, golide amasungunulira m'ng'anjo, chonchonso munthu amayesedwa ndi mbiri yake.
22
Chitsiru ngakhale uchisinje mu mtondo ndi munsi pamodzi ndi chimanga, kupusa kwake sikudzachoka konse.
23
Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako.
24
Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse?
25
Udzu ukatha, msipu nkuphuka, ndipo atatuta udzu wakumapiri,
26
anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda.
27
Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya, iweyo ndi banja lako, ndiponso ndi adzakazi ako omwe.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31