bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 30
Proverbs 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
1
Naŵa mau a Aguri, mwana wa Yake, wa ku Masa: Inu Mulungu, ine ndatopa. Inu Mulungu, ine ndatopa, ndalefukiratu.
2
Ndithudi, ine ndine wopusa koposa anthu onse. Ndilibe nzeru zonga za munthu.
3
Sindidaphunzire nzeru, ndipo Woyera uja sindimdziŵa.
4
Kodi ndani adaakwera kumwamba natsikako? Ndani adafumbatapo mphepo m'manja? Ndani adafukusapo madzi m'chovala? Ndani adakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani, ndipo mwana wake dzina lake ndani? Tanenatu ngati ukudziŵa!
5
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
6
Pa mau ake usamaonjezeko kanthu, kuwopa kuti angakudzudzule, ndipo ungapezeke kuti ndiwe wabodza.
7
Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri, musandimane zimenezo ndisanafe:
8
Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,
9
kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
10
Wantchito usamsinjirire kwa mbuyake, kuti angakutemberere, ndipo iweyo ungapezeke kuti ndiwe wolakwa.
11
Pali ena amene amatemberera atate ao, ndipo sadalitsa amai ao.
12
Pali ena amene amadziyesa oyera mtima, koma sadachotse zoipa zao.
13
Pali ena amene amadzitukumula kwambiri, amadziyesa abwino kwabasi.
14
Pali ena amene amasongola mano ao ngati malupanga, amaŵanola ngati mipeni, kuti adye amphaŵi ndi kuŵachotsa pa dziko lapansi, kutinso achotse anthu osauka pakati pa anzao.
15
Mtsundu uli ndi ana aakazi aŵiri. Anawo amangokhalira kulira kuti, “Tipatseni chakuti, tipatseni chakuti.” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta. Pali zinthu zinai zimene siziti, “Takwana.”
16
Manda, mkazi wosabala, nthaka yachiwumire ndiponso moto womangoyakirayakira.
17
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18
Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa kwambiri. Pali zinthu zinai zimene sindizimvetsa konse, zinthuzo ndi izi:
19
M'mene umaulukira mphamba mu mlengalenga, m'mene imayendera njoka pa thanthwe, m'mene chimayendera chombo pa nyanja yakuya, ndiponso m'mene mwamuna amachitira akakhala ndi namwali.
20
M'mene amachitira mkazi akachita chigololo amatere: amati akadya nkupukuta pakamwa, namanena kuti, “Palibe chimene ndalakwa.”
21
Pali zinthu zitatu zimene dziko lapansi limanjenjemera nazo. Pali zinthu zinai zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira:
22
kapolo akasanduka mfumu, chitsiru chikakhuta,
23
mkazi wonyozeka akakwatiwa, ndiponso mdzakazi akalanda malo a mbuyake.
24
Pali zinthu zinai zing'onozing'ono pa dziko lapansi, koma ndi zochenjera kwambiri:
25
Nyerere zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonzeratu chakudya chake m'chilimwe.
26
Mbira zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonza pokhala pake m'matanthwe.
27
Dzombe lilibe mfumu, komabe lonse limakhala m'magulumagulu poyenda.
28
Buluzi ungathe kumugwira ndi manja, komabe amakhala m'nyumba za mafumu.
29
Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya. Pali zinthu zinai zimene zimayenda monyadira:
30
Mkango umene uli ndi mphamvu kupambana nyama zonse, ndipo suthaŵa kanthu kalikonse.
31
Tambala woyenda chinyachinya, ndi tonde, ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32
Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza, kapena wakhala ukukonzekera kuchita zoipa, yamba wati chete, uziganize bwino.
33
Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika. Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31