bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 19
Proverbs 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
1
Wosauka amene amayenda molungama amaposa munthu wopusa wolankhula zokhota.
2
Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu, ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera.
3
Kupusa kwake kwa munthu kukamgwetsa m'chiwonongeko, mtima wake umadzakwiyira Chauta.
4
Chuma chimachulukitsa abwenzi atsopano, koma wosauka abwenzi ake amamthaŵa.
5
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6
Ambiri amafuna kuti munthu wopata aŵakomere mtima, munthu wooloŵa manja amakhala bwenzi la anthu onse.
7
Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo ndiye adzamthaŵira kunka kutali. Amayesetsa kuŵalondola mopembedzera, koma osaŵathanso.
8
Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo. Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino.
9
Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza adzaonongeka.
10
Nkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wachuma, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
11
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
12
Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
13
Mwana wopusa ndi tsoka kwa atate ake, mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi.
14
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
15
Ulesi umagonetsa tulo tofa nato, choncho munthu waulesi adzavutika ndi njala.
16
Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo, koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa.
17
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
18
Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo, ukapanda kutero, wamuwononga.
19
Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.
20
Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.
21
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
22
Chofunika kwa munthu nkukhulupirika. Kukhala wosauka nkwabwino koposa kukhala wonama.
23
Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera.
24
Waulesi amati akapisa dzanja m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake.
25
Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo. Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu, adzapindulapo nzeru.
26
Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.
27
Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mau opatsa nzeru.
28
Mboni yachabe imanyoza chilungamo, pakamwa pa anthu oipa pamalikwira tchimo.
29
Zakonzeka kale kuti mlandu uŵagwere anthu onyoza, mkwapulo ndi wokonzakonza kuti akwapulire pamsana pa zitsiru.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31