bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 7
Proverbs 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
1
Mwana wanga, mvera mau anga, malamulo anga akhale chuma chako.
2
Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako.
3
Achite ngati waŵamangirira ku chala, ngati waŵadinda mumtima mwako.
4
Nzeru uiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe la kumvetsa zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
5
Zikuteteze kwa mkazi wadama, ku mau oshashalika a mkazi wosakhala wako.
6
Tsiku lina pa windo la nyumba yanga, ndidasuzumira pa made,
7
ndipo pakati pa anthu opusa, pakati pa achinyamata, ndidaona wachinyamata mmodzi wopanda nzeru.
8
Ankayenda m'njira pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, ankaphera mu mseu wa kunyumba kumeneko.
9
Inali nthaŵi ya chisisira, madzulo, nthaŵi yausiku, kuli mdima.
10
Ndiye mkazi adadzakumana naye, atavala ngati mkazi wadama, wa mtima wonyenga.
11
Mkaziyo ndi wosakhazikika ndi wopanda manyazi, kamwendom'njira wosakhala pakhomo.
12
Mwina umpeza pa mseu, mwina pa msika, amachita kukhalizira munthu pa mphambano iliyonse.
13
Tsono amamgwira mnyamata uja, nkumumpsompsona, amalankhula naye ndi nkhope yopanda manyazi kunena kuti,
14
“Ndinayenera kupereka nsembe, ndipo lero ndachita zimene ndidazilumbirira.
15
Motero tsopano ndabwera kuti ndidzakumane nawe, ndinkakufunafuna, tsono ndakupeza.
16
Pabedi panga ndayalapo zofunda zabwino, pali nsalu zabafuta zamaŵangamaŵanga za ku Ejipito.
17
Pomweponso ndawazapo zonunkhira za mure, ndi mankhwala a fungo lokoma a aloyi, ndi a sinamoni.
18
Bwera tsono, tikhale malo amodzi mpaka m'maŵa, tisangalatsane ndi chikondi.
19
Mwamuna wanga kulibe, ali pa ulendo wautali.
20
Adatenga thumba la ndalama, adzabwerako mwezi utakhwima.”
21
Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika.
22
Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha,
23
mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo.
24
Ndiye tsopano ana inu, mundimvere ine, mutchere khutu pa zimene ndinene ine.
25
Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo, musasokere potsata njira zakezo.
26
Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri, anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka.
27
Nyumba yake ndi njira yakumanda, yotsikira ku dziko la anthu akufa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31