bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 17
Proverbs 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
1
Kuli bwino kudya mkute wouma pali bata, kuposa kuchita madyerero m'nyumba m'mene muli mikangano.
2
Kapolo wochita zinthu mwanzeru adzalamula mwana wa mfulu wochita zamanyazi, kapoloyo adzagaŵana nawo choloŵa ngati mmodzi mwa abale.
3
Siliva amamuyesera m'chitofu, golide amamuyesera m'ng'anjo, koma mitima amaiyesa ndi Chauta.
4
Wochita zoipa amamvera malangizo oipa, wabodza amamvera zochoka m'kamwa monyenga.
5
Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
6
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ulemerero wa ana ndi atate ao.
7
Kulankhula kwabwino sikuyenerana ndi chitsiru. Nanji kulankhula kwabodza, kodi kungayenerane ndi mfumu?
8
Chiphuphu chili ngati mankhwala amwai kwa wochiperekayo, kulikonse kumene amapita, amalemera.
9
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
10
Munthu wanzeru amamva kamodzi, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
11
Munthu woipa mtima amangofuna zoukira. Tsono adzamtumira wamthenga wankhalwe.
12
Kuli bwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana, kupambana kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
13
Munthu akamabwezera zoipa kwa zabwino, tsoka silidzachoka pabanja pake.
14
Chiyambi cha mkangano chili ngati kukhamulira madzi, ndiye uzichokapo ndeu isanabuke.
15
Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa, amanyansa Chauta, nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta.
16
M'manja mwa wopusa mungakhalirenji ndalama zogulira nzeru, chikhalirecho mutu wake suyenda bwino?
17
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
18
Munthu wopanda nzeru amapereka chikole, ndipo amasanduka chigwiriro pamaso pa mnzake.
19
Wokonda zolakwa amakonda mkangano. Wokonda kulankhula zonyada amadziitanira chiwonongeko.
20
Munthu wa mtima woipa zake sizimuyendera bwino. Ndipo wa pakamwa ponena zoipa amagwa m'tsoka.
21
Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, bambo wake wa chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
22
Mtima wosangalala umakhala ngati mankhwala abwino, koma mtima woziya umaumitsa thupi.
23
Munthu woipa amalandira chiphuphu cham'seri, ndipo amapotoza chigamulo cha mlandu.
24
Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru, koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse.
25
Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, ndipo amapweteka mtima wa amai ake amene adambala.
26
Kulipitsa munthu wosalakwa nkoipa. Si chilungamo kukwapula anthu abwino.
27
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
28
Nchitsiru chomwe chikakhala chete, chimakhala ngati munthu wanzeru. Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31