bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 13
Proverbs 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
1
Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.
2
Munthu wabwino amapeza nako phindu kulankhula kwake, koma anthu onyenga amalakalaka zandeu.
3
Amene amagwira pakamwa pake amasunga moyo wake, koma amene amangolakatika amaonongeka.
4
Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.
5
Munthu wokonda Mulungu amadana ndi bodza, koma zochita za munthu woipa zimanyansa ndipo zimachititsa manyazi.
6
Chilungamo chimatchinjiriza munthu wabwino, koma tchimo limagwetsa munthu woipa.
7
Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe. Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka.
8
Chuma cha munthu wolemera nchimene chimaombola moyo wake, koma munthu wosauka alibe choti nkumuwombola.
9
Kuŵala kwa anthu a Mulungu kumachita kuti ngwee, koma nyale ya anthu oipa mtima siidzalephera kuzima.
10
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
11
Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.
12
Chinthu chochiyembekeza chikalephereka, chimafooketsa mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chili ngati mtengo wopatsa moyo.
13
Wonyoza malangizo amadziwononga, koma wosamala lamulo amalandira mphotho.
14
Maphunzitso a anthu anzeru ali ngati kasupe wa moyo, amathandiza anthu kuti asakodwe mu msampha wa imfa.
15
Munthu wa nzeru zabwino, anthu amamkomera mtima, koma munthu wosakhulupirika, kwake nkuwonongeka.
16
Munthu wochenjera amachita zonse mwanzeru, koma wopusa amaonetsa poyera uchitsiru wake.
17
Wamthenga woipa amagwetsa anthu m'mavuto, koma mtumwi wokhulupirika amadzetsa mtendere.
18
Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo, koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka.
19
Chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chimasangalatsa mtima. Koma kuleka zoipa kuli ngati chinthu chonyansa kwa zitsiru.
20
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
21
Choipa chitsata mwini, koma wochita chilungamo amalandira zabwino.
22
Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.
23
M'tsala la munthu wosauka mumalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amalanda chakudyacho.
24
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.
25
Munthu wabwino ali nazo zokwanira zoti adye nkukhuta, koma m'mimba mwa munthu woipa mumakhala pululu ndi njala.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31