bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 14
Proverbs 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
1
Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma wopusa amalipasula ndi zochita zake zomwe.
2
Woyenda molungama amaopa Chauta, koma woyenda mokhotakhota amanyoza Chauta.
3
Kulankhula kwa chitsiru kumamuitanira ndodo pa msana, koma mau a munthu wanzeru amamteteza.
4
Kopanda ng'ombe, kumakhalanso kopanda dzinthu, koma kwa ng'ombe zamphamvu, dzinthu dzimachuluka.
5
Mboni yokhulupirika siinama, koma mboni yonyenga imalankhula zabodza.
6
Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.
7
Usayandikirepo pamene pali chitsiru, paja pamenepo supezapo mau anzeru.
8
Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.
9
Zitsiru sizilabadako za kulapa machimo ao, kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
10
Mtima umadziŵa wokha zoŵaŵa zake, ndipo palibe wina angadziŵe kukondwa kwake.
11
Nyumba ya munthu woipa idzapasuka, koma hema la munthu wolungama lidzakhazikika.
12
Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kopherezera kwake nku imfa.
13
Ngakhale poseka, mtima nkumvabe chisoni, ndipo mathero a chimwemwe ndi chisoni.
14
Munthu wosalungama adzalandira zoyenerera ntchito zake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito zake.
15
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.
16
Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa, koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako.
17
Munthu wopsa mtima msanga amachita zauchitsiru, wa khalidwe lonyenga, anthu amadana naye.
18
Anthu opusa wao ndi uchitsiru, koma ochenjera yao ndi mphotho ya kudziŵa zinthu.
19
Anthu ochimwa adzaŵeramira anthu abwino, anthu oipawo adzapempha thandizo kwa abwinowo.
20
Mmphaŵi ngakhale anzake omwe samukonda, koma wolemera amakhala ndi abwenzi ambiri.
21
Amene amanyoza mnzake ngwochimwa, koma ngwodala amene amachitira chifundo amphaŵi.
22
Kodi amene amakonzekera zoipa sachimwa? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amaŵaonetsa chifundo ndi kukhulupirika.
23
Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.
24
Mphotho ya anthu anzeru ndi nzeru zao zomwe, koma anthu opusa malipiro ao ndi uchitsiru wao.
25
Mboni yokhulupirika imapulumutsa anthu, koma mboni yonama imaphetsa.
26
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
27
Kuwopa Chauta ndiye kasupe wa moyo, kumapewetsa misampha ya imfa.
28
Chinamtindi cha anthu ndiye ulemerero wake wa mfumu, koma anthu akasoŵa, ufumu wake umasanduka wachabechabe.
29
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
30
Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imaoletsa mafupa.
31
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
32
Anthu ochita zoipa amatayika, koma ochita zabwino amatetezedwa.
33
Nzeru zimakhala mumtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma mumtima mwa zitsiru sizipezeka.
34
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
35
Mfumu imakondwa ndi mtumiki wochita zinthu mwanzeru, koma imakwiyira wochita zinthu mochititsa manyazi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31