bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 21
Proverbs 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
1
Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi m'manja mwa Chauta. Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna.
2
Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
3
Kuchita zolungama ndi zokhulupirika kumakondweretsa Chauta koposa kupereka nsembe.
4
Maso odzikuza ndi mtima wonyada zimatsogolera anthu oipa ngati nyale, nchifukwa chake amachimwa.
5
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
6
Chuma chomachipeza monyenga chimangoti wuzi ngati nthunzi, ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7
Ndeu za anthu oipa zidzaŵaononga, poti amakana kuchita zolungama.
8
Njira ya munthu woipa ndi yokhotakhota, koma khalidwe la munthu wosachimwa ndi lolungama.
9
Kuli bwino kukhala potero pa denga kupambana kukhala m'nyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10
Mtima wa munthu woipa umalakalaka zoipa. Samva chifundo konse ndi mnzake wovutika.
11
Munthu wonyoza akalangidwa, wopusapusa amaphunzirapo nzeru. Munthu wanzeru akamlangiza, amamvetsa zambiri.
12
Mulungu ngwachilungamo nthaŵi zonse, amadziŵa zimene anthu oipa akuchita ndipo adzawaononga.
13
Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka.
14
Mphatso yam'seri imaposa ukali, ndipo chiphuphu chosereza chimathetsa mphamvu ngakhale ya mkwiyo woopsa.
15
Chilungamo chikachitika, nzika zabwino zimakondwera, koma zimadederetsa atambwali.
16
Munthu amene amasiya njira ya anthu anzeru, adzapezeka m'gulu la anthu akufa.
17
Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.
18
Oipa adzakhala choombolera anthu abwino, ndipo osakhulupirika adzakhala choombolera anthu a mtima wabwino.
19
Kuli bwino kukhala ku chipululu kupambana kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
20
Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma munthu wopusa amachiwononga.
21
Amene amatsata chilungamo ndi chifundo adzapeza moyo ndi ulemu.
22
Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu a mphamvu, ndipo amagwetsa linga lamphamvu limene anthuwo ankalikhulupirira.
23
Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake, sapeza mavuto.
24
Munthu wonyada ndi wodzikuza amamtchula “Mnyodoli,” chifukwa amachita zinthu modzitama ndi mwachipongwe.
25
Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha, poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito.
26
Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.
27
Nsembe ya anthu oipa imamnyansa Chauta, nanji tsono akaipereka ndi cholinga choipa!
28
Mboni yonama idzaonongeka, koma mau a munthu wakumva adzamveka nthaŵi zonse.
29
Munthu woipa amafuna kuwoneka wolimba mtima, koma munthu woongoka amaganizira bwino zochita zake.
30
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
31
Kavalo amamkonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Chauta amene amapambanitsa.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31