bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 6
Proverbs 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
1
Mwana wanga, kodi udalonjeza kumlipirira mnzako chikole, kodi udaperekera mlendo chigwiriro?
2
Kodi udakodwa ndi mau a pakamwa pako pomwe, kodi udagwidwa ndi mau olankhula iwe wemwe?
3
Ndiye iwe mwana wanga, popeza kuti wadziponya m'manja mwa mnzako, chita izi kuti udzipulumutse: nyamuka, pita msanga, ukampemphe kuti akumasule.
4
Usagone tulo, usaodzere,
5
Dzipulumutse monga imadzipulumutsira mphoyo kwa mlenje, monga imadzipulumutsira kwa wosaka.
6
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru.
7
Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira.
8
Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
9
Kodi ukhalabe uli gone pamenepo mpaka liti, mlesi iwe? Kodi titha liti tulo takoto?
10
Ukati ndingogonako pang'ono, ndingoodzerako pang'ono chabe, ndingopinda manja okhaŵa kuti ndipumuleko,
11
umphaŵi udzakugwira ngati munthu wachifwamba, usiŵa udzakufikira mwadzidzidzi ngati mbala.
12
Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza.
13
Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake.
14
Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu.
15
Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse.
16
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:
17
maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
18
mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,
19
mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
20
Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako.
21
Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako.
22
Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.
23
Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu.
24
Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere.
25
Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake.
26
Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe.
27
Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa?
28
Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera?
29
Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa.
30
Paja anthu sainyoza mbala, ikaba chifukwa cha njala.
31
Komabe ikangogwidwa, imalipira kasanunkaŵiri, mpaka mwina kulandidwa katundu yense wa m'nyumba mwake.
32
Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru, amangodziwononga yekha.
33
Adzangolandira mabala ndi manyozo, ndipo manyazi ake sadzamchoka ai.
34
Paja nsanje imakalipitsa mwini mkaziyo, sachita chifundo akati alipsire.
35
Savomera dipo lililonse, sapepeseka ngakhale umpatse mphatso zochuluka chotani.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31