bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 24
Proverbs 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
1
Usamachitira nsanje anthu ochimwa, kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo,
2
chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto.
3
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu.
4
Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
5
Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.
6
Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.
7
Nzeru ndi yapatali kwambiri kwa munthu wopusa, alibe chonena pa bwalo lamilandu.
8
Amene amakonzekera kuchita choipa, adzatchedwa mvundulamadzi.
9
Kukonzekera zopusa nkuchimwa, munthu wonyoza amanyansa anthu.
10
Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa.
11
Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha.
12
Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake?
13
Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino, madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa.
14
Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
15
Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba ngati munthu woipa mtima, usachite nayo nkhondo nyumba yake.
16
Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse.
17
Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa.
18
Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo.
19
Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa.
20
Pajatu munthu woipa zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo, moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale.
21
Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu, usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano.
22
Ameneŵa amatha kugwetsa tsoka mwadzidzidzi, ndani angadziŵe kuwopsa kwa chiwonongeko chochokera kwa aŵiriŵa?
23
Enanso ndi aŵa malangizo a anthu anzeru: Kukondera pozenga milandu si chinthu chabwino.
24
Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye.
25
Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.
26
Munthu woyankha zoona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
27
Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.
28
Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, pakamwa pako pasamanena zonama.
29
Usamanena kuti, “Ndidzamchitira monga momwe iye wandichitira ine, ndidzamlipsira chifukwa cha zomwe iye wandichitira ine.”
30
Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31
M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa.
32
Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili:
33
Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,”
34
umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31