bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 25
Proverbs 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 26 →
1
Enanso ndi aŵa malangizo a Solomoni amene anthu a Hezekiya, mfumu ya ku Yuda adaŵalemba:
2
Ulemerero wa Mulungu wagona pa kubisa zinthu, m'menemo ulemerero wa mafumu wagona pa kuzifufuza zinthuzo.
3
Monga momwe uliri mlengalenga kutalika, ndi momwe liliri dziko lapansi kuzama, ndi m'mene aliri maganizo a mfumu kusadziŵika kwake.
4
Chotsa zoipa m'siliva, ndipo wosula adzatha kupanga naye chiŵiya.
5
Muchotse aphungu oipa pamaso pa mfumu, ndipo ufumu wake udzakhazikika pa chilungamo.
6
Usamadzikuza ukakhala pamaso pa mfumu, usamakhala pa malo a anthu apamwamba.
7
Pajatu kuli bwino kuchita kukuuza kuti, “Dzakhale pokwera pano”, koposa kuchita kukutsitsa chifukwa cha wina wokupambana. Zimene maso ako azipenya,
8
usafulumire kupita nazo ku bwalo lamilandu, chifukwa udzatani nanga pambuyo pake, ngati mnzako akuchititsa manyazi pokutsutsa?
9
Mnzako uzichita kukamba naye zinthu, ndipo usaulule chinsinsi cha wina,
10
kuwopa kuti wina akamva mau ako, angakuchititse manyazi, ndipo mbiri yako yoipa sidzatha.
11
Mau amodzi olankhula moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide m'choikamo chasiliva.
12
Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.
13
Kwa anthu amene amtuma, wamthenga wokhulupirika ali ngati madzi ozizira pa nthaŵi yotentha, amaziziritsa mtima wa mbuyake.
14
Munthu wonyadira mphatso imene saipereka, ali ngati mitambo ndi mphepo zopanda mvula.
15
Kupirira ndiye kumagonjetsa wolamula, ndipo kufeŵa m'kamwa kumafatsitsa mtima wouma.
16
Ukapeza uchi, ingodya wokukwanira, kuwopa kuti ungakoledwe nawo nkuyamba kusanza.
17
Kunyumba kwa mnzako uzipitako kamodzikamodzi, kuwopa kuti angatope nawe, nkuyamba kudana nawe.
18
Munthu wochitira mnzake umboni wonama, amapweteka mnzakeyo ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
19
Kukhulupirira munthu wosakhulupirika pa nthaŵi yamavuto kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa, kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka.
20
Kuimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kumvula zovala pa nyengo yachisanu, ndiponso ngati kumthira vinyo wosasa pa chilonda.
21
Mdani wako akakhala ndi njala, umpatse chakudya, akamva ludzu, umpatse madzi akumwa.
22
Potero udzamchititsa manyazi aakulu, ndipo Chauta adzakupatsa mphotho.
23
Mphepo ya mpoto ndiyo imadza ndi mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.
24
Kuli bwino kukhala potero pa denga, kupambana kukhala m'nyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
25
Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali uli ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.
26
Munthu wabwino amene amagonjera munthu woipa amafanafana ndi kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oipa.
27
Si kwabwino kudya uchi wambiri, tsono muchenjere nawo mau oyamikira.
28
Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31