bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 16
Proverbs 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
1
Zolinga zamumtima ndi za munthu, koma zolankhula zake ndi zochokera kwa Chauta.
2
Ntchito zake za munthu zimakhala zolungama pamaso pake, koma Chauta amaweruza zamumtima.
3
Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
4
Chauta adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale ndi cholinga chake, ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto.
5
Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta, ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa.
6
Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.
7
Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.
8
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.
9
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
10
M'kamwa mwa mfumu mumatuluka chigamulo chochokera kwa Mulungu. Pakamwa pa mfumu sipalakwa pogamula mlandu.
11
Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta.
12
Kuchita zoipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wao.
13
Mau oona amakondweretsa mfumu, ndipo imamkonda munthu wolankhula chilungamo.
14
Mfumu ikakwiya, ndiye kuti imfa ili pafupi, koma munthu wanzeru amaupepesa mkwiyowo.
15
Kukoma mtima kwa mfumu kumadzetsa moyo, kuli ngati mitambo ya mvula yam'chilimwe.
16
Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.
17
Mseu wa munthu wolungama umapewa zoipa. Munthu wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.
18
Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa.
19
Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.
20
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
21
Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu, kulankhula kwake kokometsera kumakulitsa mphamvu ya mau ake.
22
Nzeru ndi kasupe wopatsa moyo kwa amene ali nazo, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa anthu opusa.
23
Mtima wa munthu wanzeru umamlankhulitsa mau ochenjera, nzeruzo zimakulitsa mphamvu ya mau ake.
24
Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
25
Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa.
26
Njala ya munthu wantchito imamthandiza kulimbikira, ndi njalayo imene imamkakamiza kuchita kanthu.
27
Munthu wopandapake amakonzekera kuchita zoipa, mau ake ali ngati moto wopsereza.
28
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
29
Munthu wandeu amakopa mnzake, ndipo amamuyendetsa m'njira yoipa.
30
Amene amatsinzinira masoŵa, amalingalira zinthu zokhota, amene amachita msunamo amadzetsa zoipa.
31
Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali.
32
Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.
33
Maere amaŵaponya m'funkha, koma amene amaulula ndi Chauta.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31