bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 11
Proverbs 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
1
Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.
2
Kunyada kukaloŵa, pamafikanso manyazi, koma pali kudzichepetsa, palinso nzeru.
3
Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.
4
Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.
5
Kulungama kwa anthu angwiro kumaŵathandiza pa moyo wao, koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo.
6
Kulungama kwa munthu woyera mtima kumampulumutsa, koma zilakolako zoipa zimaŵaika mu ukapolo anthu onyenga.
7
Woipa akafa, chikhulupiriro chake chimathanso, chiyembekezo cha wosasamala za Mulungu chilibe phindu.
8
Anthu a Mulungu amapulumuka ku mavuto, koma m'malo mwake amagwamo ndi oipa mtima.
9
Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu.
10
Mulungu akamadalitsa anthu ake, mzinda wonse umatukuka. Oipa akaonongeka, anthu amafuula mwachimwemwe.
11
Madalitso olandira anthu olungama amakweza mzinda, koma pakamwa pa anthu oipa mtima pamapasula mzindawo.
12
Wosukitsa anzake ngwopanda nzeru, koma womvetsa zinthu amalonda pakamwa pake.
13
Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
14
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
15
Woperekera wachilendo chigwiriro, adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chigwiriro, amakhala pa mtendere.
16
Mkazi wa mkhalidwe wabwino amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.
17
Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino, koma munthu wankhwidzi amadzipweteka yekha.
18
Munthu woipa amalandira malipiro achabechabe, koma wochita zolungama amalandira mphotho yeniyeni.
19
Wofunitsitsa chilungamo, adzakhala moyo. Koma wothamangira zoipa, adzafa.
20
Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta, koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa.
21
Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya, koma anthu a Mulungu adzapulumuka.
22
Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
23
Zimene anthu abwino amazilakalaka zimathera mwabwino, koma zimene oipa amayembekezera zimathera ku mkwiyo wa Mulungu.
24
Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.
25
Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.
26
Anthu amatemberera munthu womana anzake chakudya, koma amalemekeza munthu wogulitsa chakudyacho.
27
Munthu wofunafuna zabwino mwakhama, amapeza zokoma, koma wofunafuna zoipa, zidzampeza.
28
Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.
29
Wovutitsa a m'nyumba mwake adzaloŵa m'mavuto, chitsiru chidzasanduka kapolo wa munthu wanzeru.
30
Kukhala moyo wangwiro kumapezetsa moyo, koma kusatsata malamulo kumaononga moyo.
31
Anthu abwino amalandira mphotho pa dziko lapansi, koma wochimwa ndi woipa mtima amalandira chilango.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31