bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 15
Proverbs 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
1
Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.
2
Mau a anthu anzeru amapatsa nzeru, koma pakamwa pa opusa pamatulutsa zauchitsiru.
3
Maso a Chauta ali ponseponse, amayang'ana oipa ndi abwino omwe.
4
Mau ofatsa amakhala ngati mtengo wopatsa moyo, koma mau oipa amapweteka mtima.
5
Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake, koma wochenjera amamvera chidzudzulo.
6
Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri, koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto.
7
Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru, koma mitima ya zitsiru siitero.
8
Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.
9
Zochita za anthu oipa zimamnyansa Chauta, koma wochita zachilungamo Chauta amamkonda.
10
Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Amene amadana ndi kudzudzula adzafa.
11
Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika kwa Mulungu, nanji tsono mitima ya anthu!
12
Wonyada sakonda kumdzudzula, sapitako kwa anthu anzeru.
13
Mtima wosangalala umaonetsa nkhope yachimwemwe, koma mtima wachisoni umaphwanya moyo.
14
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
15
Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthaŵi zonse.
16
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.
17
Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.
18
Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.
19
Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga, koma njira ya munthu wolungama imakhala ngati mseu wosalala.
20
Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
21
Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amatsata zolungama.
22
Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.
23
Kuyankha mokhoza kumakondwetsa munthu, ndipo mau onena pa nthaŵi yake amakoma.
24
Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.
25
Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.
26
Maganizo a anthu oipa amamnyansa Chauta, koma mau a anthu olungama amamkondweretsa.
27
Munthu wofunafuna phindu monyenga amavutitsa banja lake, koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino.
28
Munthu wabwino amaganizira za m'mene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woipa pamatuluka mau oipa okhaokha.
29
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
30
Maso okondwa amasangalatsa mtima, ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.
31
Amene makutu ake amalandira bwino kudzudzula koyenera, adzakhala m'gulu la anthu anzeru.
32
Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.
33
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31