bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 31
Proverbs 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
1
Naŵa mau a mfumu Lemuwele wa ku Masa amene adamphunzitsa mai wake:
2
Nchiyani, mwana wanga? Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga? Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita kukupempha polonjeza ndi malumbiro?
3
Mphamvu zako usathere pa akazi, usamayenda nawo ameneŵa, amaononga ndi mafumu omwe.
4
Iwe Lemuwele, mafumu sayenera kumamwa vinyo, olamulira asamalakalaka zakumwa zaukali,
5
kuwopa kuti angaiŵale malamulo a dziko, ndi kukhotetsa zinthu zoyenerera anthu osauka.
6
Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.
7
Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake asakumbukirenso kuvutika kwake.
8
Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera.
9
Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.
10
Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.
11
Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu.
12
Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.
13
Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
14
Ali ngati zombo za anthu amalonda, zakudya zake amakazitenga kutali.
15
Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake.
16
Amalingalira za munda, naugula. Amalima munda wamphesa ndi ndalama zozipeza ndi manja ake.
17
Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito.
18
Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse.
19
Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha.
20
Anthu osauka amaŵachitira chifundo, amphaŵi amaŵapatsa chithandizo.
21
A pabanja pake saŵaopera kuti nkufa nacho chisanu, poti amadziŵa kuti onsewo amavala zovala zofunda.
22
Amadzipangira yekha zofunda, ndipo iye amavala zovala zabafuta ndi za mtengo wapatali.
23
Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko.
24
Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
25
Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala.
26
Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma.
27
Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe.
28
Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati,
29
“Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”
30
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
31
Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31