bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 20
Proverbs 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
1
Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.
2
Mkwiyo woopsa wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango. Amene amauputa dala mkwiyowo, amataya moyo wake.
3
Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.
4
Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera. Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu, koma sadzapeza kanthu.
5
Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi ozama, ndi munthu wanzeru yekha angazitulutse.
6
Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao, koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika kwenikweni?
7
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
8
Pamene mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imazindikira ndi maso chabe anthu onse amene ali oipa.
9
Ndani angathe kunena kuti, “Ine ndauyeretsa mtima wanga, ndilibenso tchimo lililonse.”
10
Masikelo ndi miyeso ina yoyesera zinthu zikakhala zonyenga, zonsezo zimamunyansa Chauta.
11
Ngakhale mwana yemwe amadziŵika ndi ntchito zake, kuti zimene amachitazo ndi zabwino ndi zolungama.
12
Makutu amene timamvera ndiponso maso amene timapenyera, zonsezo adazilenga ndi Chauta.
13
Usakondetse tulo, kuwopa kuti ungagwe mu umphaŵi. Khala maso, ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
14
Munthu akamagula kumene chinthu amati, “Nchoipa, nchoipa,” koma atagula nkuchokapo, amayamba kudzitama.
15
Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.
16
Munthu amene waperekera mlendo chikole, umlande chovala chake, chimenecho chikhale chigwiriro chako, chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika.
17
Chakudya chochipeza monyenga chimamkomera munthu, koma pambuyo pake chimakasanduka ngati lubwe m'kamwa mwake.
18
Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.
19
Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
20
Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.
21
Choloŵa chopata mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pambuyo pake.
22
Usamanena kuti, “Ndidzabwezera choipa ndine.” Udikire Chauta, ndipo adzakuthandiza.
23
Miyeso yosintha imanyansa Chauta, masikelo onyenga ndi oipanso.
24
Mayendedwe a munthu amaŵalamula ndi Chauta: Tsono munthu angadziŵe bwanji njira yake?
25
Ndi msampha kwa munthu kupereka chinthu kwa Chauta mosaganiza bwino, chifukwa mwina atha kusintha maganizo atalumbira kale.
26
Mfumu yanzeru imazindikira oipa, ndipo imaŵalanga mopanda chisoni.
27
Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.
28
Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.
29
Kukongola kwa achinyamata kwagona pa nyonga zao, koma ulemerero wa nkhalamba wagona pa imvi zao.
30
Mikwingwirima ndiye mankhwala ochotsa zoipa. Mikwapulo imachiza zam'katikati mwa munthu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31