bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 12
Proverbs 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
1
Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.
2
Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Chauta, koma munthu wokonzekera zoipa, Chauta amamzenga mlandu.
3
Munthu sakhazikika bwino pochita uchimo, koma maziko a munthu wochita zabwino sadzagwedezeka.
4
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
5
Maganizo a munthu wabwino ngoongoka, koma malangizo a munthu woipa ngonyenga.
6
Mau a munthu woipa mtima ngophetsa, koma mau a munthu wolungama ngopulumutsa anthu.
7
Anthu oipa mtima amagwetsedwa, naiŵalika, koma banja la anthu omvera Mulungu silidzapasuka.
8
Munthu amamuyamika malinga ndi nzeru zake, koma munthu wa mtima wokhota amanyozeka.
9
Munthu wamba, wodzigwirira ntchito napeza zofunika, ali pabwino kuposa wongodzikuza, pamene alibe nchakudya chomwe.
10
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
11
Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
12
Nsanja yolimba ya anthu oipa mtima imaonongeka, koma maziko a munthu wabwino ngosagwedezeka.
13
Munthu woipa amakodwa mu msampha wa zoipa za pakamwa pake, koma munthu wochita zabwino amapulumuka ku zoipa.
14
Munthu amalandira zabwino zambiri chifukwa cha mau ake abwino, ntchito zimene munthu amazichita ndi manja ake zimampindulira.
15
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
16
Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.
17
Wolankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yonama imalankhula monyenga.
18
Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
19
Mau oona amakhala mpaka muyaya, koma zabodza sizikhalitsa.
20
Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.
21
Munthu wabwino vuto silimgwera, koma woipa mavuto samchoka.
22
Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.
23
Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma anthu opusa amaonetsa poyera kupusa kwao.
24
Ogwira ntchito mwakhama adzakhala olamulira, koma aulesi adzakhala akapolo.
25
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
26
Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.
27
Munthu waulesi sapeza zimene akukhumba, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengowapatali.
28
Njira ya chilungamo imafikitsa ku moyo, koma njira ya zoipa imafikitsa ku imfa.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31