bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 22
Proverbs 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
1
Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.
2
Wolemera ndi wosauka akulingana, pakuti onsewo adaŵalenga ndi Chauta.
3
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
4
Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta, ndi chuma, ulemu ndi moyo.
5
M'njira ya munthu wosalungama muli minga ndi misampha, koma wodzisamala bwino adzazilewa zonsezo.
6
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
7
Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.
8
Amene amabzala kusalungama adzakolola mavuto, ndipo ndodo ya ukali wake idzathyoka.
9
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
10
Mukampirikitsa wonyoza, kukangana kudzatha, ndipo ndeu ndi zonyoza zidzalekeka.
11
Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kulankhula zabwino, adzakhala bwenzi la mfumu.
12
Chauta amayang'anira bwino anthu odziŵa zinthu, koma mau a anthu osakhulupirika, Iye amaŵalepheretsa.
13
Waulesi amati, “Pali mkango pabwalopo! Ndikaphedwa m'miseu.”
14
Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.
15
Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.
16
Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.
17
Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.
18
Chidzakhala chokondwetsa ukazisunga, ndi kukhala wokonzeka kumazilankhula pa nthaŵi yake.
19
Ndakudziŵitsa zimenezi lero kuti makamaka iweyo uzikhulupirira Chauta.
20
Kodi suja ndidakulembera malangizo makumi atatu, okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21
malangizo okudziŵitsa zolungama ndi zoona, kuti ukaŵayankhe zoona amene adakutuma?
22
Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu.
23
Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.
24
Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali,
25
kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.
26
Usakhale mmodzi mwa anthu opereka zikole, amene amasanduka chigwiriro cha ngongole.
27
Ngati ulephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.
28
Usasendeze malire akalekale amene makolo ako adaŵaika.
29
Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31