bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 29
Proverbs 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 30 →
1
Munthu wochita liwuma kwina atamdzudzula, adzaonongeka mwadzidzidzi osachiranso.
2
Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa, koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula.
3
Wokonda nzeru amasangalatsa atate ake, koma amene amayenda ndi akazi adama amamwaza chuma chake.
4
Mfumu imalimbitsa dziko pakuweruza molungama, koma imene imaumiriza anthu kuti aipatse ziphuphu, imaononga dziko.
5
Munthu amene amathyasika mnzake amadzitchera msampha yekha.
6
Munthu woipa amakodwa ndi zolakwa zake, koma wochita chilungamo amakhala wokondwa ndi womasuka.
7
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
8
Anthu onyoza akhoza kuyatsa mzinda, koma anthu anzeru amabweza ukali.
9
Munthu wanzeru atatsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso nkumaseka, ndipo sipakhala mtendere.
10
Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wosalakwa, koma anthu angwiro amateteza moyo wake.
11
Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.
12
Wolamula akamamvera zabodza, nduna zake zonse zidzakhala zoipa.
13
Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanafana pa ichi, chakuti onsewo Chauta ndiye adaŵapatsa maso.
14
Mfumu ikamaweruza osauka mosakondera, ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya.
15
Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
16
Oipa akamalamulira, zolakwa zimachuluka, koma ochita chilungamo adzaona kugwa kwa oipawo.
17
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
18
Kumene kulibe mithenga yochokera kwa Mulungu, anthu saweruzika, ndi wodala munthu amene amatsata malamulo.
19
Munthu wotumikira samulanga ndi mau chabe, ngakhale aŵamvetse mauwo, sadzasamalako.
20
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
21
Amene amasasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana, pomaliza pake adzapeza kuti kapoloyo wasanduka mloŵachuma wake.
22
Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.
23
Kunyada kwa munthu kudzamtsitsa, koma amene ali wodzichepetsa adzalandira ulemu.
24
Woyenda ndi mbala ndi wodana ndi moyo wake, amamva kutemberera, koma osaulula kanthu.
25
Kuwopa anthu kuli ngati msampha, koma wodalira Chauta amakhala pabwino.
26
Ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira aŵakomere mtima, koma munthu amamuweruza molungama ndi Chauta yekha.
27
Anthu osoŵa chilungamo amanyansa anthu ochita chilungamo, monga momwe anthu abwino amanyansira anthu oipa mtima.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31