bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 10
Proverbs 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
1
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
2
Chuma chochipeza monyenga sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
4
Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu.
5
Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.
6
Madalitso amakhala pa munthu wokondweretsa Mulungu, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.
7
Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso, pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola.
8
Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
9
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
10
Munthu wotsinzinira maso monyenga, amadzetsa mavuto, wodzudzula molimba mtima amadzetsa mtendere.
11
Pakamwa pa munthu wabwino ndi kasupe wa moyo, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.
12
Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13
Pakamwa pa munthu womvetsa zinthu pamatuluka zanzeru, koma pamsana pa munthu wopanda nzeru sipachoka tsatsa.
14
Anzeru amakundika nzeru, koma kubwebwetuka kwa chitsiru kumadzetsa chiwonongeko.
15
Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake, koma umphaŵi wa anthu osauka ndiye chiwonongeko chao.
16
Moyo ndiye malipiro a anthu ochita zabwino, koma phindu la ochimwa limadzetsa machimo ena.
17
Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera.
18
Wobisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo wochita ugogodi nchitsiru.
19
Mau akachuluka, zolakwa sizisoŵa, koma amene amasunga pakamwa ndi wanzeru.
20
Mau a munthu wochita zabwino, ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma maganizo a anthu oipa ngachabe.
21
Mau a anthu wabwino amaphunzitsa ambiri, koma zitsiru zimafa chifukwa chosoŵa nzeru.
22
Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23
Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
24
Chimene woipa amachiwopa chidzamgwera, koma zimene munthu wabwino amazilakalaka adzazipeza.
25
Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa, koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya.
26
Momwe amakhalira vinyo wosasa m'kamwa, momwe umakhalira utsi m'maso, ndi momwenso amakhalira mlesi kwa amene amamtuma.
27
Kuwopa Chauta kumatalikitsa moyo, koma zaka za anthu oipa zidzachepa.
28
Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe, koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira.
29
Chauta ndi linga loteteza munthu woyenda molungama, koma amaononga wochita zoipa.
30
Munthu wabwino sadzachotsedwa pamalo pake, koma woipa sadzakhazikika pa dziko.
31
Pakamwa pa wochita chilungamo pamatuluka zanzeru, koma lilime lokhota adzalidula.
32
Anthu omvera Mulungu amadziŵa zoyenera kulankhula, koma pakamwa pa anthu oipa pamatuluka zosayenera.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31