bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Proverbs 5
Proverbs 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 6 →
1
Mwana wanga, umvetsere bwino zanzeru ndikukuuzazi, utchere khutu kwa ine womvetsa bwino zinthu,
2
kuti uziganiza mochenjera, ndipo pakamwa pako pazilankhula zanzeru.
3
Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta.
4
Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5
Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda.
6
Njira yamoyo saisamala mpang'ono pomwe. Njira zake nzokhotakhota, koma mwiniwakeyo sadziŵako.
7
Tsopano, ana inu, mundimvere ine, musaŵataye mau a pakamwa panga.
8
Uzilambalala kutali ndi mkazi wotere, usamafika kufupi ndi khomo la nyumba yake.
9
Mwinamwina ulemu wako udzalanditsa kwa ena, zaka zako zaunyamata udzazitaya kwa anthu ankhanza.
10
Mwinanso alendo adzadyerera chuma chako, phindu la ntchito zako lidzagwa m'manja mwa munthu wachilendo.
11
Ndipo potsiriza pa moyo wako udzalira chokuwa, thupi lako lonse litatheratu.
12
Pamenepo iwe udzangoti, “Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo, mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13
Sindidamvere mau a aphunzitsi anga, sindidatchere khutu kwa alangizi anga.
14
Pang'onong'ono, bwenzi nditaonongekeratu pakati pa mpingo wonse utasonkhana.”
15
Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako.
16
Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu?
17
Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo.
18
Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako.
19
Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.
20
Mwana wanga, ungakopekerenji ndi mkazi wadama, ungamkumbatire bwanji mkazi wosakhala wako?
21
Mayendedwe a munthu Chauta amaŵaona bwino lomwe, njira zake zonse amazipenyetsetsa.
22
Zoipa za munthu woipa zimamtchera msampha iyeyo, ntchito za machimo ake zimamkwidzinga.
23
Amafa chifukwa chosoŵa mwambo, amatayika chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31