bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 10
Proverbs 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
1
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.
2
Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.
3
Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.
4
Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5
Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakutula ndi mwana wochititsa manyazi.
6
Madalitso ali pamtu pa wolungama; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
7
Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.
8
Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo; koma chitsiru cholongolola chidzagwa.
9
Woyenda moongoka amayenda osatekeseka; koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.
10
Wotsinzinira achititsa chisoni; koma wodzudzula momveka achita mtendere.
11
M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
12
Udani upikisanitsa; koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.
13
Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira; koma wopusa pamsana pake nthyole.
14
Anzeru akundika zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.
15
Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphawi wao uononga osauka.
16
Ntchito za wolungama zipatsa moyo; koma phindu la oipa lichimwitsa.
17
Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera.
18
Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.
19
Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.
20
Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika; koma mtima wa oipa uli wachabe.
21
Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; koma zitsiru zimafa posowa nzeru.
22
Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.
23
Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24
Chomwe woipa achiopa chidzamfikira; koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.
25
Monga kavumbulu angopita, momwemo woipa kuli zii; koma olungama ndiwo maziko osatha.
26
Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso, momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma.
27
Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.
28
Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.
29
Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzaonongeka.
30
Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m'dziko.
31
M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32
Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31