bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 19
Proverbs 19
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
1
Wosauka woyenda mwangwiro aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.
2
Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.
3
Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.
4
Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri; koma mnzake wa waumphawi amleka.
5
Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6
Ambiri adzapembedza waufulu; ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.
7
Abale onse a wosauka amuda; nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye? Awatsata ndi mau, koma kuli zii.
8
Wolandira nzeru akonda moyo wake; wosunga luntha adzapeza zabwino.
9
Mboni yonama sidzapulumuka chilango; wolankhula mabodza adzaonongeka.
10
Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka; nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?
11
Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.
12
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.
13
Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake; ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.
14
Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.
15
Ulesi ugonetsa tulo tofa nato; ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.
16
Wosunga lamulo asunga moyo wake; wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.
17
Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.
18
Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga.
19
Munthu waukali alipire mwini; pakuti ukampulumutsa udzateronso.
20
Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.
21
Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.
22
Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake; ndipo wosauka apambana munthu wonama.
23
Kuopa Yehova kupatsa moyo; wokhala nako adzakhala wokhuta; zoipa sizidzamgwera.
24
Waulesi alonga dzanja lake m'mbale, osalibwezanso kukamwa kwake.
25
Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera; nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
26
Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.
27
Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo.
28
Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo; m'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa.
29
Akonzera onyoza chiweruzo, ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31