bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 12
Proverbs 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
1
Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.
2
Yehova akomera mtima munthu wabwino; koma munthu wa ziwembu amtsutsa.
3
Munthu sadzakhazikika ndi udyo, muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
5
Maganizo a olungama ndi chiweruzo; koma uphungu wa oipa unyenga.
6
Mau a oipa abisalira mwazi; koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.
7
Oipa amagwa kuli zii; koma banja la olungama limaimabe.
8
Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.
9
Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo, aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.
10
Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.
11
Zakudya zikwanira wolima minda yake; koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.
12
Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu; koma muzu wa olungama umabala zipatso.
13
M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.
14
Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.
15
Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.
16
Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa; koma wanzeru amabisa manyazi.
17
Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo; koma mboni yonama imanyenga.
18
Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.
19
Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.
20
Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa; koma aphungu a mtendere amakondwa.
21
Palibe vuto lidzagwera wolungama; koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.
22
Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.
23
Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa; koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24
Dzanja la akhama lidzalamulira; koma waulesi adzakhala ngati kapolo.
25
Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mau abwino aukondweretsa.
26
Wolungama atsogolera mnzake; koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27
Waulesi samaotcha nyama yake anaigwira; koma wolungama amalandira chuma chopambana cha anthu.
28
M'khwalala la chilungamo muli moyo; m'njira ya mayendedwe ake mulibe imfa.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31