bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 22
Proverbs 22
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
1
Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.
2
Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova.
3
Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.
4
Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.
5
Minga ndi misampha ili m'njira ya wokhota; koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.
6
Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.
7
Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.
8
Wofesa zosalungama adzakolola tsoka; ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.
9
Mwini diso lamataya adzadala; pakuti apatsa osauka zakudya zake.
10
Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka; makani ndi manyazi adzalekeka.
11
Wokonda kuyera mtima, mfumu idzakhala bwenzi lake chifukwa cha chisomo cha milomo yake.
12
Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.
13
Waulesi ati, Pali mkango panjapo, ndidzaphedwa pamakwalalapo.
14
M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.
15
Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.
16
Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.
17
Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.
18
Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako, ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.
19
Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi, kuti ukhulupirire Yehova.
20
Kodi sindinakulembera zoposa za uphungu ndi nzeru;
21
kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?
22
Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.
23
Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.
24
Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;
25
kuti ungaphunzire mayendedwe ake, ndi kutengera moyo wako msampha.
26
Usakhale wodulirana mpherere, ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake.
27
Ngati ulibe chobwezera kodi achotserenji kama lako pansi pako?
28
Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire, chimene makolo ako anachiimika.
29
Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31