bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 26
Proverbs 26
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
1
Monga chipale chofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika, momwemo ulemu suyenera chitsiru.
2
Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.
3
Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham'kamwa chiyenera bulu, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.
4
Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti ungafanane nacho iwe wekha.
5
Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti asadziyese wanzeru.
6
Wotumiza mau ndi dzanja la chitsiru adula mapazi ake, namwa zompweteka.
7
Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
8
Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala, momwemo wochitira chitsiru ulemu.
9
Monga munga wolasa dzanja la woledzera, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
10
Monga woponya mivi ndi kulasa onse, momwemo wolembera chitsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira.
11
Monga galu abweranso kumasanzi ake, momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake.
12
Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru? Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai.
13
Waulesi ati, Mkango uli panjira, wobangulawo uli m'makwalala.
14
Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu, momwemo waulesi agubuduka pakama pake.
15
Waulesi alonga dzanja lake m'mbale; kumtopetsa kulibweza kukamwa kwake.
16
Waulesi adziyesa wanzeru koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.
17
Wakungopita ndi kuvutika ndi ndeu yosakhala yake akunga wogwira makutu a galu.
18
Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa,
19
momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku.
20
Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka.
21
Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto; momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.
22
Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka zitsikira m'kati mwa mimba.
23
Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.
24
Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake.
25
Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26
Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.
27
Wokumba dzenje adzagwamo, wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.
28
Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31