bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 7
Proverbs 7
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
1
Mwananga, sunga mau anga, ukundike malangizo anga,
2
Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.
3
Uwamange pa zala zako, uwalembe pamtima pako.
4
Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongo wanga; nutche luntha mbale wako.
5
Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.
6
Pakuti pa zenera la nyumba yanga ndinapenyera pamwamba pake; ndinaona pakati pa achibwana,
7
ndinazindikira pakati pa ang'ono mnyamata wopanda nzeru,
8
alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, ndi kuyenda pa njira ya kunyumba yake;
9
pa madzulo kuli sisiro, pakati pa usiku pali mdima.
10
Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira, atavala zadama wochenjera mtima,
11
ali wolongolola ndi wosaweruzika, mapazi ake samakhala m'nyumba mwake.
12
Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, nabisalira pa mphambano zonse.
13
Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona; nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe,
14
nsembe zamtendere zili nane; lero ndachita zowinda zanga.
15
Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira, kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.
16
Ndayala zofunda pakama panga, nsalu zamawangamawanga za thonje la ku Ejipito,
17
ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni.
18
Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamawa; tidzisangalatse ndi chiyanjano.
19
Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali;
20
watenga thumba la ndalama m'dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21
Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.
22
Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru;
23
mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
24
Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mau a m'kamwa mwanga.
25
Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo, usasochere m'mayendedwe ake.
26
Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi.
27
Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira kuzipinda za imfa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31