bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 3
Proverbs 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
1
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;
2
pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
3
Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako;
4
motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;
6
umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
7
Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;
8
mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi.
9
Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;
10
motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo.
11
Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;
12
pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.
13
Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha;
14
pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka.
15
Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.
16
Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere.
17
Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.
18
Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.
19
Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha.
20
Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake; thambo ligwetsa mame.
21
Mwananga, zisachokere kumaso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;
22
ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.
23
Pompo udzayenda m'njira yako osaopa, osaphunthwa phazi lako.
24
Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa.
25
Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa;
26
pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.
27
Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.
28
Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.
29
Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.
30
Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa.
31
Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.
32
Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.
33
Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama.
34
Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo.
35
Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31