bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 6
Proverbs 6
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
1
Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole, ngati wapangana kulipirira mlendo,
2
wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako, wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.
3
Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse; popeza walowa m'dzanja la mnzako, pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako.
4
Usaone tulo m'maso mwako, ngakhale kuodzera zikope zako.
5
Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki, ndi mbalame kudzanja la msodzi.
6
Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere;
7
zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu;
8
koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; nizituta dzinthu zao m'masika.
9
Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka kutulo tako liti?
10
Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;
11
ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.
12
Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota.
13
Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake;
14
zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.
15
Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.
16
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:
17
Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;
18
mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;
19
mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
20
Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako;
21
uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako.
22
Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka.
23
Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.
24
Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.
25
Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake.
26
Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali.
27
Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?
28
Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake?
29
Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.
30
Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala;
31
koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.
32
Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.
33
Adzalasidwa nanyozedwa; chitonzo chake sichidzafafanizidwa.
34
Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.
35
Sadzalabadira chiombolo chilichonse, sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31