bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 21
Proverbs 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
1
Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.
2
Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.
3
Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.
4
Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, ndi nyali ya oipa, zili tchimo.
5
Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.
6
Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7
Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola; chifukwa akana kuchita chiweruzo.
8
Wosenza tchimo njira yake ikhotakhota; koma ntchito ya woyera mtima ilungama.
9
Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
10
Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa; sakomera mtima mnzake.
11
Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru, naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.
12
Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu, kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.
13
Wotseka makutu ake polira waumphawi, nayenso adzalira koma osamvedwa.
14
Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo, ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.
15
Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu.
16
Munthu wosochera pa njira ya nzeru adzakhala m'msonkhano wa akufa.
17
Wokonda zoseketsa adzasauka; wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18
Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama; ndipo wachiwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.
19
Kukhala m'chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.
20
Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; koma wopusa angozimeza.
21
Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.
22
Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba, nagwetsa mphamvu yake imene anaikhulupirira.
23
Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.
24
Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza; achita mwaukali modzitama.
25
Chifuniro cha waulesi chimupha; chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.
26
Ena asirira modukidwa tsiku lonse; koma wolungama amapatsa osamana.
27
Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.
28
Mboni yonama idzafa; koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika.
29
Munthu woipa aumitsa nkhope yake; koma woongoka mtima akonza njira zake.
30
Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.
31
Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31