bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 23
Proverbs 23
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 24 →
1
Pamene ukhala ulinkudya ndi mkulu, zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;
2
nuike mpeni pakhosi pako, ngati uli wadyera.
3
Usakhumbe zolongosoka zake; pokhala zakudya zonyenga.
4
Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.
5
Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.
6
Usadye zakudya zake za wa maso ankhwenzule, ngakhale kukhumba zolongosoka zake.
7
Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.
8
Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza, ndi kutaya mau ako okondweretsa.
9
Usalankhule m'makutu a wopusa; pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.
10
Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire; ngakhale kulowa m'minda ya amasiye;
11
pakuti Mombolo wao walimba; adzawanenera mlandu wao pa iwe.
12
Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mau anzeru.
13
Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai.
14
Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.
15
Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa.
16
Imso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka.
17
Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.
18
Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
19
Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m'njiramo.
20
Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.
21
Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.
22
Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba.
23
Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.
24
Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
25
Atate wako ndi amai ako akondwere, amai ako akukubala asekere.
26
Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.
27
Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza.
28
Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu.
29
Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?
30
Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.
31
Usayang'ane pavinyo alikufiira, alikung'azimira m'chikho, namweka mosalala.
32
Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba.
33
Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.
34
Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.
35
Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31