bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 15
Proverbs 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
1
Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.
2
Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.
3
Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino.
4
Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo.
5
Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.
6
M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri; koma m'phindu la woipa muli vuto.
7
Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama.
8
Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.
9
Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo.
10
Wosiya njira adzalangidwa mowawa; wakuda chidzudzulo adzafa.
11
Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?
12
Wonyoza sakonda kudzudzulidwa, samapita kwa anzeru.
13
Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.
14
Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa; koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.
15
Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.
16
Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.
17
Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.
18
Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.
19
Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga, koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.
20
Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake.
21
Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.
22
Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.
23
Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake; ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino?
24
Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.
25
Yehova adzapasula nyumba ya wonyada; koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake.
26
Ziwembu zoipa zinyansa Yehova; koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.
27
Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.
28
Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.
29
Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.
30
Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima; ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.
31
Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo lidzakhalabe mwa anzeru.
32
Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.
33
Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31