bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 14
Proverbs 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
1
Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.
2
Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m'njira yake amnyoza.
3
M'kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza; koma milomo ya anzeru idzawasunga.
4
Popanda zoweta modyera muti see; koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu.
5
Mboni yokhulupirika sidzanama; koma mboni yonyenga imalankhula zonama.
6
Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.
7
Pita pamaso pa munthu wopusa, sudzazindikira milomo yakudziwa.
8
Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
9
Zitsiru zinyoza kupalamula; koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.
10
Mtima udziwa kuwawa kwakekwake; mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.
11
Nyumba ya oipa idzapasuka; koma hema wa oongoka mtima adzakula.
12
Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.
13
Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.
14
Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake; koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
15
Wachibwana akhulupirira mau onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.
16
Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka.
17
Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.
18
Achibwana amalandira cholowa cha utsiru; koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.
19
Oipa amagwadira abwino, ndi ochimwa pa makomo a olungama.
20
Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka.
21
Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala.
22
Kodi oganizira zoipa sasochera? Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.
23
M'ntchito zonse muli phindu; koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.
24
Korona wa anzeru ndi chuma chao; utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25
Mboni yoona imalanditsa miyoyo; koma wolankhula zonama angonyenga.
26
Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.
27
Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, kupatutsa kumisampha ya imfa.
28
Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; koma popanda anthu kalonga aonongeka.
29
Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.
30
Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.
31
Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.
32
Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.
33
Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira, nidziwika pakati pa opusa.
34
Chilungamo chikuza mtundu wa anthu; koma tchimo lichititsa fuko manyazi.
35
Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru; koma idzakwiyira wochititsa manyazi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31