bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 31
Proverbs 31
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
1
Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa.
2
Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga? Chiyani mwana wa zowinda zanga?
3
Musapereke mphamvu yako kwa akazi, ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.
4
Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?
5
Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.
6
Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali, ndi vinyo kwa owawa mtima;
7
amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake.
8
Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse.
9
Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.
10
Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale.
11
Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu.
12
Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.
13
Afuna ubweya ndi thonje, nachita mofunitsa ndi manja ake.
14
Akunga zombo za malonda; nakatenga zakudya zake kutali.
15
Aukanso kusanake, napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito.
16
Asinkhasinkha za munda, naugula; naoka mipesa ndi zipatso za manja ake.
17
Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake.
18
Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku.
19
Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake.
20
Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake.
21
Saopera banja lake chipale chofewa; pakuti banja lake lonse livala mlangali.
22
Adzipangira zimbwi zamawangamawanga; navala bafuta ndi guta wofiirira.
23
Mwamuna wake adziwika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko.
24
Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa ogulitsa malonda.
25
Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo.
26
Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.
27
Ayang'anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi.
28
Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati,
29
Ana akazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo.
30
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.
31
Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31