bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 11
Proverbs 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
1
Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.
2
Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.
3
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.
4
Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.
5
Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake; koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.
6
Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
7
Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka; chiyembekezo cha uchimo chionongeka.
8
Wolungama apulumuka kuvuto; woipa nalowa m'malo mwake.
9
Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.
10
Olungama akapeza bwino, mudzi usekera; nufuula pakuonongeka oipa.
11
Madalitso a olungama akuza mudzi; koma m'kamwa mwa oipa muupasula.
12
Wopeputsa mnzake asowa nzeru; koma wozindikira amatonthola.
13
Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mau.
14
Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.
15
Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo; koma wakuda chikole akhala ndi mtendere.
16
Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; aukali nagwiritsa chuma.
17
Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.
18
Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.
19
Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha.
20
Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.
21
Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango; koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.
22
Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
23
Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha; koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.
24
Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.
25
Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26
Womana tirigu anthu amtemberera; koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.
27
Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero; koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28
Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29
Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru.
30
Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru.
31
Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno; koposa kotani woipa ndi wochimwa?
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31